Pitani ku nkhani yake

Khoti Lalikulu mzinda wa Mutare ku Zimbabwe. Mkati (kuchokera kumanzere kupita kumanja) M’bale Jabulani Sithole, Wonder Muposheri ndi Tobias Gabaza

18 NOVEMBER, 2022
ZIMBABWE

Khoti Lalikulu ku Zimbabwe Lagamula Mokomera a Mboni za Yehova pa Nkhani ya Ufulu Wachipembedzo

Khoti Lalikulu ku Zimbabwe Lagamula Mokomera a Mboni za Yehova pa Nkhani ya Ufulu Wachipembedzo

Pa 29 September 2022, Khoti Lalikulu mu mzinda wa Mutare ku Zimbabwe, linagamula mokomera M’bale Tobias Gabaza, Wonder Muposheri komanso M’bale Jabulani Sithole, omwe ankasalidwa chifukwa chokana kutenga nawo mbali pamwambo wa chipembedzo womwe ndi wosemphana ndi zomwe amakhulupirira.

Mu October 2020, abale atatuwa anaitanidwa kuti akaonekere pamaso pa mfumu ya m’mudzi wawo, atakana zimene mmodzi mwa akuluakulu a m’mudzimo anawalamula, kuti atenge nawo mbali pamwambo wina womwe unkachitika m’mudzimo. Mwambowo unkaphatikizapo kupempha mizimu ya anthu akufa kuti iwabweretsere mvula ndipo munthu wina aliyense wa m’mudzimo ankayenera kutengapo mbali. Abale athuwa anakana kuti atenge nawo mbali pa mwambowu mogwirizana ndi chikumbumtima chawo chophunzitsidwa bwino Baibulo.

Mfumuyo inagamula kuti abalewa anali olakwa ndipo inayesetsa kuwakakamiza kuti atenge nawo mbali pamwambowo. Choncho abale athuwa anasankha zopanga apilo nkhaniyi ku Khoti Laling’ono ku Chipinge m’dzikolo.

Ndiyeno pa 5 January, 2021, khotili linagamula mokomera abalewa. Komabe, akuluakulu a m’mudzimo anakana kutsatira zimene khotili linagamula ndipo anapitiriza kuvutitsa abalewa. Kuonjezera pamenepo, anthu enanso a m’mudzimo anayamba kusala komanso kunyoza abalewa.

Ndiye chifukwa choti anthu ankapitiriza kunyoza abalewa, iwo anaganiza zopanga apilo nkhaniyi ku Khoti Lalikulu. Khotili linapeza kuti akuluakulu a m’mudziwo ankaphwanya ufulu wa abalewa. Ndipo linalamula akuluakuluwo kuti alipire abalewo komanso kuti asamawakakamize kutenga nawo mbali pamwambo wa chikhalidwe uliwonse womwe ndi wosemphana ndi zimene amakhulupirira.

Tikukhulupirira kuti chigamulo chimenechi chithandiza abale ndi alongo onse m’dziko la Zimbabwe chifukwa miyambo ngati imeneyi imachitika m’dziko lonselo. Ndipo tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha chigamulochi.—Miyambo 2:8.