Pitani ku nkhani yake

APRIL 12, 2021
ZAMBIA

Kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Achigiriki M’chilankhulo cha Chimambwe-Lungu

Kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Achigiriki M’chilankhulo cha Chimambwe-Lungu

Pa 3 April 2021 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Achigiriki la pa zipangizo za makono linatulutsidwa m’chilankhulo cha Chimambwe-Lungu. M’bale Albert Musonda, wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Zambia, ndi amene anatulutsa Baibulo limeneli pa pulogalamu yochita kujambula yomwe abale ndi alongo a ku Zambia komanso ku Tanzania anaonerera. Chilankhulo cha Chimambwe-Lungu chimalankhulidwa ndi ofalitsa 2,531 a ku Zambia komanso ofalitsa 325 a ku Tanzania, kumene chimadziwikanso kuti Chifipa.

Timu ya abale atatu ndi imene inagwira ntchito yomasulira Baibuloli kwa miyezi 21. Mmodzi mwa abale amene ankamasulira nawo ananena kuti anthu ena ankaona kuti Baibulo lakale la Chimambwe- Lungu linali lovuta kuwerenga chifukwa linali ndi mawu achikale. Koma pofotokoza za Baibulo lomwe longotulutsidwa kumeneli, omasulira winanso ananena kuti: “M’Baibulo latsopanoli muli mawu amene anthu amagwiritsira ntchito polankhulana tsiku lililonse.”

Sitikukayikira kuti mphatso yapadera yochokera kwa Yehova imeneyi ithandiza anthu ambiri amene amalankhula Chimambwe-Lungu kuti azisangalala ndi kuwerenga mawu ouziridwa a Mulungu.—Salimo 1:2.