Pitani ku nkhani yake

14 NOVEMBER 2022
ZAMBIA

Baibulo La Dziko Latsopano Linatulutsidwa M’Chimbunda

Baibulo La Dziko Latsopano Linatulutsidwa M’Chimbunda

Pa 5 November 2022, M’bale Cephas Kalinda wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Zambia, anatulutsa Baibulo la Dziko latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu mu Chimbunda. Baibuloli linatulutsidwa pa pulogalamu yochita kujambulidwa imene anthu oposa 1,500 anamvetsera ndipo Baibulo la pazipangizo za makono linayamba kupezeka nthawi yomweyo. Ma Baibulo ochita kusindikizidwa adzayamba kupezeka mu January 2023.

Chilankhulo cha Chimbunda chimalankhulidwa kwambiri ku Angola ndi ku Zambia. A Mboni za Yehova anayamba kulalikira anthu oyankhula Chimbunda m’zaka za m’ma 1930 ku Northern Rhodesia (panopa Zambia). Mu 2014, kagulu komasulira Chimbunda kanakhazikitsidwa. Ma ofesi a omasulira chinenerochi ali ku Mongu m’chigawo chakumadzulo kwa Zambia.

Ma ofesi a omasulira Chisilozi ndi Chimbunda ku Mongu m’dziko la Zambia

Kupatulapo pa Baibulo la Dziko latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu, kuli Baibulo limodzi lokha la Chimbunda koma ndi lokwera mtengo komanso lovuta kumvetsa. Chifukwa cha zimenezi, abale ndi alongo olankhula Chimbunda amagwiritsa ntchito ma Baibulo a Dziko Latsopano a m’zilankhulo zina.

Ponena za Baibulo latsopanoli, mmodzi mwa anthu amene anamasulira ananena kuti: “Ndi lomveka bwino komanso losavuta kuwerenga ndipo chofunika kwambiri n’chakuti linatanthauzira choonadi cha m’Baibulo molondola.”

Pofotokoza za mavuto amene ankakumana nawo polalikira akamagwiritsa ntchito Baibulo la Chimbunda limodzi lokha lija, womasulira wina anati: “Munalibe dzina la Yehova ngakhale pa vesi limodzi. M’malomwake anaikamo dzina la udindo lakuti ‘Ambuye Mulungu wathu’ ponena za Yehova. Zimenezi zimapangitsa kuti zikhale zovuta kwa anthu kuti adziwe dzina la Mulungu. Koma Baibulo lathu latsopanoli, linagwiritsa ntchito dzina lakuti Yehova maulendo okwana 237.”

Tili ndi chikhulupiriro kuti Baibulo latsopanoli lithandiza abale ndi alongo olankhula Chimbunda kuti alimbitse chikhulupiriro chawo mwa Yehova komanso kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi iye.