Pitani ku nkhani yake

Ngakhale kuti nthawi zambiri ku Ukraine sikukumakhala magetsi, zimenezi sizikumalepheretsa abale athu kuti asamapezeke pamisonkhano. Kumanzere: Oyang’anira dera akukamba nkhani kukagulu ka ofalitsa ka mpingo kunyumba ya m’bale. M’mwamba kumanja: Misonkhano ikuchitikabe ku Nyumba ya Ufumu ngakhale kuti kulibe magetsi. M’munsi kumanja: Banja likuchita misonkhano kudzera pa Zoom pa nthawi yomwe kulibe magetsi

20 DECEMBER 2022
UKRAINE

LIPOTI #14 | Abale Akupitiriza Kukondana pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

LIPOTI #14 | Abale Akupitiriza Kukondana pa Nthawi Yankhondo ku Ukraine

Zinthu zambiri za ku Ukraine monga misewu, mabiliji komanso malo opanga magetsi zaonongeka kapena kuonongekeratu chifukwa cha mabomba amene akuphulika kawirikawiri. Ngakhale zili choncho, abale athu sanasiyebe kupezeka pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito za Ufumu ngakhale kuti nthawi zambiri kukumakhala kopanda magetsi.

Kupezeka pamisonkhano ya pa Zoom pa nthawi yomwe kulibe magetsi

Anastasia ndi Debora omwe amachita upainiya ku Kyiv, ananena kuti amakhala tsiku lonse lathunthu opanda magetsi. Amatchaja zipangizo zawo zamakono pa nthawi yomwe angakwanitse komanso kugwiritsa ntchito mayunitsi amufoni yawo kuti azipezeka pamisonkhano. Nthawi zambiri Intaneti imavuta kwambiri misonkhano ikatha.

Vuto linanso lomwe amakumana nalo chifukwa cha kuzima kwa magetsi ndi kuvutika kugwiritsira ntchito zipangizo zotenthetsera mpweya. Kuti akhale ndi magetsi komanso kugwiritsira ntchito zipangizo zotenthetsera mpweya, ena mwa abale akumagwiritsa ntchito majenereta. Ndipo abale ena akukhala ndi achibale awo omwe ali ndi zotenthetsera mpweya m’nyumba zawo pomwe ena amapirira kuzizirako. Koma chosangalatsa n’chakuti m’nyumba zambiri za abale muli zipangizo zotenthetsera mpweya zomwe amagwiritsa ntchito gasi, choncho sizidalira magetsi.

Iryna yemwe ndi mpainiya ku Ivano-Frankivsk, amayesetsa kuona zinthu moyenerera. Iye ananena kuti, “Ndinaganiza zoti ndisamaganizire kwambiri za zinthu zimene sindingathe kuzisintha. Ndiye ndimangochita zomwe ndingathe paola limenelo basi. Ndimaganizira zomwe ndingachite pa nthawi yomwe magetsi azima ndipo ndimaonetsetsa kuti ndapangiratu dawunilodi mabuku ndi zinthu zina zofunikira pasadakhale.”

Ngakhale kuti abale ndi alongo athu akukumana ndi mavuto ambiri ku Ukraine, iwo akuyesetsabe kuchita zambiri potumikira Yehova. Ndife otsimikiza kuti Iye apitiriza kudalitsa khama lawo pomwe ‘akuchita zabwino.’​—Agalatiya 6:9.

Pofika pa 6 December 2022, tinalandira malipoti otsatirawa kuchokera ku Ukraine. Ziwerengerozi zinatsimikiziridwa ndi abale am’dzikolo. Komabe n’kutheka kuti ziwerengerozi ndi zokwera kwambiri kuposa pamenepa chifukwa sitikutha kulankhulana ndi abale am’zigawo zonse za dzikolo.

Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

 • Ofalitsa 47 anafa

 • Ofalitsa 97 anavulala

 • Ofalitsa 11,537 anathawa m’nyumba zawo

 • Nyumba 590 zinawonongekeratu

 • Nyumba 645 zinawonongeka kwambiri

 • Nyumba 1,722 zinawonongeka pang’ono

 • Nyumba za Ufumu 7 zinawonongekeratu

 • Nyumba za Ufumu 19 zinawonongeka kwambiri

 • Nyumba za Ufumu 68 zinaonongeka pang’ono

Ntchito Yopereka Chithandizo

 • Pali Makomiti Othandiza pa Ngozi za Mwadzidzidzi okwana 27 omwe akugwira ntchito ku Ukraine

 • Anthu 54,212 anathandizidwa ndi makomitiwa kuti athawire kumalo otetezeka

 • Ofalitsa 26,811 anathawira kumayiko ena komwe akuthandizidwa ndi Akhristu anzawo