Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Selim Taganov

NOVEMBER 24, 2020
TURKMENISTAN

M’bale Taganov Wamasulidwa Pambuyo Pomaliza Kugwira Ukaidi kwa Chaka Chimodzi ku Turkmenistan

M’bale Taganov Wamasulidwa Pambuyo Pomaliza Kugwira Ukaidi kwa Chaka Chimodzi ku Turkmenistan

M’bale Selim Taganov atatulutsidwa m’ndende pa 3 October 2020 ananena kuti: “Pamene ndinkapemphera kwa Yehova, ankandithandiza kukhala wodekha.” Selim ali ndi zaka 19 zokha ndipo anagwira ukaidi kwa chaka chimodzi chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

Selim anabadwira mumzinda wa Ashgabat womwe ndi likulu la dziko la Turkmenistan. Ali mwana, ankakonda kuphunzira zinthu ndipo anayamba kukonda nyimbo. Selim amalemba nyimbo, amaimba komanso amatha kuimba gitala. Makolo ake, azichimwene ake awiri komanso anzake amanena kuti Selim ndi munthu wachifundo, wodekha ndiponso wansangala. Khoti lisanagamule mlandu wake, loya amene anamuimira ananena kuti: “Ndi mnyamata wabwino komanso wachilungamo ndipo sasuta kapena kumwa mowa mwauchidakwa. Wangomaliza kumene maphunziro akusekondale. Kumuika m’ndende ndi kungomulakwira.”

Moyo wakundende unali wovuta koma Selim ananena kuti: “Pa nthawi yomwe ndakhala m’ndendeyi ubwenzi wanga ndi Yehova walimba kwambiri. Ndinkakumbukira mfundo za choonadi cha m’Baibulo zomwe ndinkaphunzira pa nthawi imene ndinali kunyumba ndipo ndinayamba kuzimvetsa kwambiri. Ndikamakumbukira malemba monga la Yesaya 41:10, 11 ankandilimbikitsanso kwambiri.”

“Pa nthawi imene ndinali kumalo ena odikirira kuti mlandu wanga uzengedwe ndinavutika kwambiri chifukwa kunalibe munthu woti n’kumuuzako mmene ndikumvera. Koma ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize. Kenako ndinangoona kuti akaidi komanso oyang’anira ndende omwe poyamba ankandivutitsa komanso kundiopseza ayamba kundilimbikitsa. Zonsezi zinkanditsimikizira kuti Yehova akundithandiza.”

Abale ndi alongo nawonso ankamulimbikitsa Selim. Iye akufotokozanso kuti: “Nditaikidwa m’ndende, abale ndi alongo ambiri ankanditumizira moni komanso kundilembera mfundo zolimbikitsa. Ndinayesetsa kuloweza mfundo zomwe ankandilemberazo n’kumaziyankhula mobwerezabwereza. Zinandilimbikitsa kwambiri ndi kunditonthoza.”

Malinga ndi malamulo a dziko la Turkmenistan, Selim atha kuitanidwanso kuti akalowe usilikali. Ngati zimenezi zingachitike, Selim akudziwa kuti atha kukakhala kundende kwa nthawi yocholukirapo. Iye akunena kuti: “Pambuyo pothandizidwa ndi Yehova kuti ndipirire, pano sindikuopanso kuikidwa m’ndende. Yehova amathandiza ndipo zimenezi zikundipatsa mphamvu komanso zikundilimbitsa mtima.”

Tonsefe tikudziwa kuti tikumana ndi mayesero m’tsogolomu. Ndiye Selim akutilimbikitsa kuti: “Kwa amene angadzakumane ndi mayesero ngati angawa, osadzaiwala mawu a pa Yesaya 30:15, omwe amati: ‘Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.’”