Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Azamatjan Narkuliyev

FEBRUARY 19, 2021
TURKMENISTAN

M’bale Azamatjan Narkuliyev wa Zaka 20 Wamangidwanso Patangotha Chaka Chimodzi Atamasulidwa

M’bale Azamatjan Narkuliyev wa Zaka 20 Wamangidwanso Patangotha Chaka Chimodzi Atamasulidwa

Chigamulo

Pa 18 January 2021, khoti la ku Turkmenistan linapereka chigamulo pa mlandu wa M’bale Azamatjan Narkuliyev. Khotili linagamula kuti m’baleyu akakhale kundende ya chitetezo chokhwima kwambiri kwa zaka ziwiri pa mlandu wokana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chake. Umenewu ndi ulendo wachiwiri kuti m’baleyu amangidwe chifukwa chokana kulowa usilikali.

Zokhudza M’baleyu

Azamatjan Narkuliyev

  • Chaka chobadwa: 2000

  • Mbiri yake: Anabatizidwa mu 2018. Ali ndi mbiri yabwino pa nkhani ya kudzichepetsa komanso ndi wakhama. Mayi ake komanso achemwali ake awiri nawonso ndi a Mboni za Yehova.

Mlandu Wake

Nthawi yoyamba imene Azamatjan, wa zaka 20, anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chake, anakhala m’ndende kwa chaka chimodzi ndipo anamasulidwa pa 7 January, 2020. Koma chifukwa chakuti ku Turkmenistan munthu akhoza kumangidwanso kachiwiri ngati atakana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chake, m’baleyu anaitanidwanso kukalowa usilikali patangotha miyezi 5 atamasulidwa. Iye analemba chikalata chosonyeza kuti akukana kulowa usilikali wonyamula zida kapenanso wosanyamula zida. Koma akuluakuluwo sanavomereze pempho lake.

Pa 20 December 2020, boma linamutsegulira mlandu wina komanso linamulanda pasipoti yake.

Tikupempherera Azamatjan ndi anthu a m’banja la kwawo, tikudziwa kuti Yehova adzawadalitsa chifukwa cha mtima wawo wofunitsitsa kukhalabe okhulupirika. Baibulo limatitsimikizira kuti “munthu wokhulupirika [Yehova adzamuchitira] mokhulupirika.”—Salimo 18:25.