Turkmenistan
Dziko la Turkmenistan Linagamula Kuti a Bahram Hemdemov Akhale M’ndende Zaka 4 Chifukwa cha Chipembedzo
Apolisi anaphwanya malamulo posokoneza msonkhano umene unkachitikira m’nyumba ya a Bahram Hemdemov. Akuluakulu a makhoti anachitanso zinthu mopanda chilungamo.
Dziko la Turkmenistan Latulutsa M’ndende a Mboni Omwe Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira
Pa October 22, 2014, Pulezidenti Berdimuhamedov analamula kuti a Mboni za Yehova 8 omwe anamangidwa chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira atulutsidwe m’ndende.
Mayi Wina Watulutsidwa Kundende M’dziko la Turkmenistan
Bibi Rahmanova anatulutsidwa m’ndende mwadzidzidzi pa September 2, 2014. Ngakhale kuti mayiko ndi mabungwe ena anadandaula za nkhaniyi, oweruza sanathetse mlanduwu.
Mayi wa Mwana Wazaka 4 ku Turkmenistan Amuweruza Mopanda Chilungamo Kuti Akakhale Kundende
Dziko la Turkmenistan limakonda kuchitira nkhanza a Mboni za Yehova komanso kuwaphwanyira ufulu wachibadwidwe. Mayi Bibi Rahmanova ndi banja lawo akuchitiridwa zopanda chilungamo ndi akuluakulu a boma a ku Dashoguz.