10 FEBRUARY 2023
TURKEY
Anthu Masauzande Ambiri Akhudzidwa Ndi Chivomerezi Champhamvu ku Turkey
Lolemba m’mawa pa 6 February 2023, chivomerezi champhamvu zokwana 7.8 chinachitika kum’mwera chakum’mawa kwa Turkey. Pambuyo pake, chivomerezi chinanso champhamvu zokwana 7.5 chinachitika m’dera lomwelo. Zivomerezi zinanso zing’onozing’ono zakhala zikuchitika m’deralo. Anthu oposa 21,000 anafa ndipo enanso oposa 74,000 anavulala.
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu ku Turkey
N’zachisoni kuti mlongo wina wachikulire mumzinda wa Adana anafa pangoziyi
M’bale wina, mkazi wake, mwana wawo komanso wachibale wawo adakali kunsi kwa nyumba imene yagwa mumzinda wa Adiyaman
Nyumba zitatu zinawonongekeratu
Nyumba 17 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 17 zinawonongeka pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka kwambiri
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Abale amene akuyang’anira ntchito yothandiza anthu akulimbikitsa mwauzimu abale ndi alongo amene akhudzidwa ndi ngoziyi.
Makomiti Othandiza pa Ngozi za Mwadzidzidzi awiri anakhazikitsidwa kuti ayang’anire ntchito yopereka chithandizo
M’bale wa m’Komiti ya Nthambi akulimbikitsa mwauzimu abale ndi alongo kuphatikizapo omwe nyumba zawo zawonongekeratu kapena kuwonongeka
Ziwerengero zili pamwambazi zikusonyeza malipoti atsopano.
Ngakhale kuti abale ndi alongo athu akhudzidwa ndi chivomerezi chochititsa manthachi komanso zivomerezi zina zing’onozing’ono, iwo akulimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova ndi “pothawira pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.”—Salimo 46:1.