Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 5, 2019
TAIWAN

Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Linatulutsidwa M’Chitchainizi

Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Linatulutsidwa M’Chitchainizi

Pa 5 July, 2019, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso la Chitchainizi linatulutsidwa pamsonkhano wachigawo mumzinda wa Taoyuan ku Taiwan. M’bale Kenneth Cook wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene anatulutsa Baibuloli pamene anakamba nkhani pa bwalo la masewera la National Taiwan Sport University Stadium. Anthu 12,610, kuphatikizapo ena omwe ankaonera msonkhanowu kuchokera m’malo 4 osiyanasiyana, analipo pamene chilengezo chosaiwalika cha kutulutsidwa kwa Baibuloli chinkaperekedwa.

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chitchainizi linafalitsidwa koyamba mu 1995 ndipo linafalitsidwa la mitundu iwiri. Baibulo lina linalembedwa m’zilembo za Chitchainizi cha nthawi zonse chomwe chimagwiritsidwa ntchito kwambiri ku Hong Kong ndi ku Taiwan. Pomwe Baibulo lina linalembedwa m’zilembo za Chitchainizi chosavuta kumva chomwe chimagwiritsidwa ntchito kwambiri ku China, Malaysia, ndi ku Singapore. Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu linatulutsidwa mu 2001, la mitundunso iwiri, lina la Chitchainizi cha nthawi zonse ndi lina la Chitchainizi chosavuta kumva. Baibulo la mtundu wachitatu linatulutsidwa mu 2004. Baibuloli linalembedwa pogwiritsa ntchito zilembo za Chitchainizi zosavuta kumva zomwe zinalembedwanso mu afabeti ya Chingelezi, ndipo kalembedwe kameneka kamatchedwa kuti Pinyin.

Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso nalonso linatulutsidwa m’mitundu itatu. Mabaibulo a Chitchainizi cha nthawi zonse komanso chosavuta kumva akupezeka ochita kusindikizidwa komanso ena a pazipangizo zamakono. Pomwe Baibulo la Pinyin limapezeka pa Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI.

Pali anthu oposa 1.1 biliyoni omwe amayankhula Chitchainizi cha Chimandarini monga chinenero chawo chobadwira, ndipo Chimandarini n’chimene chili ndi anthu ambiri padziko lonse omwe ndi chinenero chawo chobadwira. Kuonjezera pa anthu omwe amayankhula Chimandarini, palinso anthu mamiliyoni ambiri omwe amayankhula Chitchainizi cha mitundu yosiyanasiyana amenenso amagwiritsa ntchito zilembo za Chitchainizi cha Chimandarini powerenga. Abale ndi alongo athu omwe akulalikira m’gawo la Chitchainizi lomwe ndi lalikulu, tsopano akhoza kugwiritsa ntchito Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso pothandiza anthu ambiri kuti adziwe Yehova komanso kuti adziwe Mawu ake molondola.—1 Timoteyo 2:4.