11 OCTOBER 2024
SPAIN
Khoti Lalikulu Loona za Ufulu wa Anthu Lagamula Kuti a Mboni za Yehova Ali ndi Ufulu Wosankha Thandizo Lachipatala Lomwe Akufuna
Oweruza Onse Anagwirizana pa Mlandu wa Pakati pa Boma la Spain ndi a Pindo Mulla
Pa 17 September 2024, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linagamula kuti wodwala aliyense ali ndi ufulu wosankha thandizo lachipatala limene akufuna mogwirizana ndi zimene amakhulupirira. Chigamulo chapaderachi sichikupita ku dziko la Spain lokha, koma mayiko onse 46 omwe ali m’Bungwe la Mayiko a ku Europe.
A Rosa Pindo Mulla ndi amuna awo a Armando
Mu June 2018, Mlongo Rosa Pindo Mulla, yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 47, anagonekedwa pachipatala china ku Madrid ku Spain kuti alandire thandizo lachipatala lomwe linali laling’ono. Asanayambe kumuthandiza, Mlongo Rosa anapereka kwa madokotala khadi lomwe anali atalilemba kale lofotokoza zimene anasankha pa nkhani ya thandizo lachipatala lomwe angalandire komanso anawafotokozera momveka bwino kuti chifukwa cha zimene amakhulupirira ndiponso chikumbumtima chake chophunzitsidwa bwino Baibulo, sangalore kuikidwa magazi. (Machitidwe 15:28, 29) Anthu a pachipatalachi analemba zimenezi mu faelo yake. Koma mlongoyu asakudziwa, oweruza wina analamula madokotala kuti amupange opaleshoni yaikulu komanso kuti amuike magazi. Atamaliza kumupanga opaleshoniyo, Mlongo Rosa anakhumudwa kwambiri atazindikira kuti madokotalawo sanamvere zomwe anawauza kuti asamuike magazi.
Popereka chigamulo pa mlanduwu, oweruza onse 17 ananena kuti “wodwala aliyense wamkulu ali ndi ufulu wokana” thandizo lachipatala limene sakulifuna, ndipo anawonjezera kuti: “Limodzi mwa malamulo ofunika kwambiri pa nkhani ya thandizo lachipatala, ndi loti madokotala akuyenera kumalemekeza ufulu wa wodwala wolandira kapena kukana thandizo lililonse lachipatala.”
Abale ndi alongo tonse padziko lapansi, tikusangalala kwambiri ndi chigamulo cha khotili chomwe chateteza ufulu wa Mlongo Pindo Mulla limodzi ndi anthu enanso mamiliyoni wosankha thandizo lachipatala logwirizana ndi zimene amakhulupirira.

