NKHANI

Overview

Chichewa
Overview
/assets/ct/7e6416ec85/images/syn_placeholder_sqr.png

SOUTH KOREA

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku South Korea

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku South Korea

A Mboni za Yehova akhala akupezeka ku Korea kwa zaka zoposa 100 ndipo akhala akulambira Mulungu mwaufulu. Vuto lalikulu limene a Mboni akumana nalo kwa nthawi yaitali ku South Korea ndi kuzengedwa milandu ndi boma chifukwa chokana ntchito yausilikali potsatira zimene amakhulupirira.

Boma la South Korea silipatsa anthu ufulu wokana ntchito yausilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndipo dzikoli lilibe lamulo loti anthuwa azipatsidwa ntchito zina. Choncho, anyamata a Mboni omwe amakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira amapatsidwa chilango choti akhale m’ndende miyezi 18. Mwezi uliwonse amuna 40 kapena 50 a Mboni amatsekeredwa m’ndende. Akatulutsidwa m’ndendemo, iwo amakumananso ndi mavuto ena chifukwa choti amakhala ndi mbiri yoti anapalamulapo mlandu ndipo amaonedwa kuti anazemba usilikali. A Mboniwa amavutika kuti apeze ntchito ndiponso amakumana ndi mavuto osiyanasiyana akafuna kuchita zinthu za tsiku ndi tsiku.

Nawonso amuna amene amaliza kugwira ntchito yausilikali mochita kuwakakamiza, amakumana ndi mavuto akaphunzira Baibulo n’kudziwa mfundo yoti akuyenera kukonda anthu ena komanso yoti sakuyenera kuphunzira nkhondo. Akakhala pamndandanda wa anthu omwe angaitanidwe kuti akagwire ntchito yausilikali ngati angafunike, azibambowo amazengedwa milandu komanso kuwalipitsa chindapusa chifukwa chokana kuchita maphunziro a ntchito yausilikali.

Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu yapereka zigamulo zoposa 500 zodzudzula boma la South Korea chifukwa chophwanya ufulu wa anthu okana usilikali potsatira zimene amakhulupirira, ndipo komitiyi imanena kuti anthuwa amatsekeredwa m’ndende “popanda zifukwa zomveka.” Komitiyi inanenanso kuti boma la South Korea “likuyenera kupewa kuphwanyira anthu ufulu mwa njira imeneyi” m’tsogolomu. Kuthetsa nkhaniyi kungathandize kuti ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima komanso wachipembedzo, uzilemekezedwa ku South Korea.