Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Omasulira m’Chinenero Chamanja cha ku Rwanda akujambula vidiyo mu ofesi yawo.

JANUARY 10, 2019
RWANDA

Ofesi ya Nthambi ku Rwanda Yayamba Ntchito Yomasulira M’chinenero Chamanja cha M’dzikolo

Ofesi ya Nthambi ku Rwanda Yayamba Ntchito Yomasulira M’chinenero Chamanja cha M’dzikolo

Chakumapeto kwa mwezi wa September mu 2018, a Mboni za Yehova ku Rwanda anachita chinthu chosaiwalika pa ntchito yawo yoyesetsa kulalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu a ziyankhulo zosiyanasiyana m’dzikolo. Pa nthawiyi anayamba ntchito yomasulira m’Chinenero Chamanja cha ku Rwanda. Ntchitoyi ithandiza abale ndi alongo pafupifupi 113 a ku Rwanda omwe ali ndi vuto losamva, komanso ithandiza kwambiri ofalitsa kuti athe kulalikira kwa anthu oposa 30,000 omwe ali ndi vuto losamva.

Omasulira m’Chinenero Chamanja cha ku Rwanda anamasulira kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha, kavidiyo kakuti Nchifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo, komanso timapepala tambiri tomwe tili m’gulu la Zinthu Zophunzitsira. Zinthuzi ziyamba kupezeka pawebusaiti yathu yovomerezeka milungu ikubwerayi.

Omasulira m’Chinenero Chamanja cha ku Rwanda amagwirira ntchito yawo pamalo ena omwe ali pamtunda woyenda 5 minitsi kuchokera pa ofesi ya nthambi ya ku Rwanda yomwe ili ku Kigali. Pa omasulirawa pali abale awiri ndi alongo awiri, ndipo mmodzi mwa abalewa ali ndi vuto losamva. Abale ndi alongo onsewa amadziwa bwino chinenero chamanja ndipo anapanga maphunziro a ntchito yomasulira omwe anachitika kwa milungu 4 ndipo cholinga cha maphunzirowa chinali kuwathandiza mmene angamagwirire ntchito yomasulirayi.

Ofesi ya omasulira m’Chinenero Chamanja cha ku Rwanda yomwe ili pafupi ndi ofesi ya nthambi ya ku Rwanda.

A Rwakibibi Jean Pierre omwe ndi mmodzi mwa omasulira m’Chinenero Chamanja cha ku Rwanda, anafotokoza chifukwa chomwe chimapangitsa ntchito yomasulira m’chinenero chamanja kukhala yovuta kwambiri kusiyana ndi kumasulira m’chinenero chochita kulemba. Iwo anati: “Anthu a vuto losamva amalankhulana pogwiritsa ntchito manja ndi nkhope, choncho omasulira m’chinenero chamanja amamasulira mawu n’kuwapanga kuti akhale vidiyo pogwiritsa ntchito njira inayake yapadera. Timakhala ndi bolodi loyera lomwe timajambulapo zithunzi zogwirizana ndi nkhani yomwe ili m’Chingelezi. Zithunzizi zimathandiza kuti nkhaniyo imasuliridwe m’chinenero chamanja mogwirizana ndi mmene ilili ku Chingelezi. Pofuna kutsimikizira kuti nkhaniyo yamasuliridwa molondola komanso momveka bwino, timaitana abale ndi alongo angapo a vuto losamva omwe sanamasulire nawo nkhaniyo kuti aonere zomwe tamasulirazo n’kufotokoza maganizo awo.”

A Augustin Munyangeyo omwe ndi tcheyamani wa bungwe loona za ufulu wa anthu a vuto losamva ku Rwanda.

A Augustin Munyangeyo omwe ndi tcheyamani wa bungwe lina lomwe si la boma lomwe limaona za ufulu wa anthu a vuto losamva ku Rwanda, anafotokoza maganizo awo pa ntchito yomasulira m’chinenero chamanja yomwe a Mboni akugwira ku Rwanda. Iwo anati: “Tikuyamikira kwambiri a Mboni za Yehova chifukwa chophunzitsa anthu mawu a Mulungu pogwiritsa ntchito Baibulo komanso mavidiyo m’Chinenero Chamanja cha ku Rwanda.”

Pofika pano, a Mboni za Yehova padziko lonse akumasulira m’zinenero zamanja zoposa 90 ndipo anapanga pulogalamu yaulere ya JW Library Sign Language® yomwe imathandiza anthu kuonera mavidiyo ofotokoza Baibulo m’zinenero zamanja zoposa 90. Kupezeka kwa mavidiyo a m’zinenero zamanja zambiri kukuthandiza abale ndi alongo athu padziko lonse kulengeza uthenga wabwino “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.”—Chivumbulutso 14:6.