Pitani ku nkhani yake

M’bale Sergey Sushilnikov

31 AUGUST, 2022
RUSSIA

“Yehova Wandipatsa Anzanga Opanda Mantha”

“Yehova Wandipatsa Anzanga Opanda Mantha”

Posachedwa Khoti la Novokuznetsk m’Boma la Kuznetsk, m’Chigawo cha Kemerovo lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Sergey Sushilnikov. Loya waboma sananene chilango chomwe akufuna kuti khotili lipereke kwa m’baleyu.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. November 2019

  Apolisi anayamba kumvetsera zimene M’bale Sushilnikov ankalankhula ndi anthu pa foni yake komanso kuona mavidiyo omwe kamela yapanyumba pa m’baleyu inajambula

 2. 3 June, 2021

  Mlandu unatsegulidwa

 3. 8 June, 2021

  Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba ndipo a Sushilnikov ndi akazi awo anawatenga ndi kukawafunsa mafunso

 4. 15 July, 2021

  Anawalemba pamndandanda wa anthu ochita zinthu zoopsa ndipo ma akaunti awo a kubanki anatsekedwa

 5. 8 February, 2022

  Anawaimba mlandu wotsogolera gulu lochita zinthu zoopsa ndipo anawauza kuti asapange ulendo ulionse wotuluka m’dzikolo

 6. 30 March, 2022

  Mlandu unayamba kuzengedwa

Zokhudza M’baleyu

Timalimbikitsidwa kudziwa kuti nthawi zonse Yehova adzapereka thandizo kwa atumiki ake okhulupirika “pa nthawi ya masautso.”—Salimo 46:1.