Pitani ku nkhani yake

Mlongo Olga Zhelavskaya

17 JANUARY 2023
RUSSIA

“Yehova Amakhala Nane Nthawi Zonse”

“Yehova Amakhala Nane Nthawi Zonse”

Posachedwa khoti la Chelyabinsk m’boma la Metallurgicheskiy lipereka chigamulo chake pa mlandu wokhudza Mlongo Olga Zhelavskaya. Loya waboma sananene chilango chomwe akufuna kuti khoti lipereke kwa mlongoyu.

Zokhudza Mlongoyu

Ndife otsimikiza mtima kuti kaya atumiki a Yehova akumana ndi mavuto otani, iwo ‘sadzagwedezeka’ ndipo timayamikira chifukwa Iye amatithandiza.​—Salimo 16:8.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 16 June 2018

  Apolisi anayamba kumvetsera zimene Mlongo Zhelavskaya ankalankhulana ndi anthu pa foni yake komanso kuona mavidiyo omwe kamera yapanyumba pake imajambula.

 2. 26 March 2019

  Apolisi anakafufuza zinthu kunyumba kwa Mlongo Zhelavskaya chifukwa cha M’bale Vladimir Suvorov yemwe ankafufuzidwanso

 3. 31 August 2021

  Anawatsegulira mlandu othandizira gulu lochita zinthu zoopsya polola kuti gululi lizichitira misonkhano kunyumba kwake

 4. 22 October 2021

  Anagonekedwa kuchipatala atagwidwa ndi sitiroko

 5. 28 September 2022

  Mlandu unayamba kuzengedwa