Pitani ku nkhani yake

M’bale Yuriy Yakovlev

9 SEPTEMBER, 2022
RUSSIA

“Ndine Wosangalala Kwambiri . . . Kuposa Kale Lonse”

“Ndine Wosangalala Kwambiri . . . Kuposa Kale Lonse”

Posachedwa khoti la Mzinda wa Sosnovoborsk womwe uli m’Chigawo cha Krasnoyarsk lipereka chigamulo pa mlandu wa M’bale Yuriy Yakovlev. Loya waboma sananene chilango chomwe akufuna kuti m’baleyu apatsidwe.

Nthawi Komanso Zomwe Zinachitika

 1. June mpaka December 2021

  Apolisi ankamvetsera zomwe a Yakovlev ankalankhulana ndi anthu pafoni yawo komanso ankaonerera zomwe kamera yawo yapanyumba inkajambula ndi cholinga chowapezera mlandu

 2. 28 March, 2022

  Anawatsegulira mlandu wochititsa msonkhano wa bungwe lochita zinthu zoopsa kudzera pa vidiyokomfelensi. Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba ya a Yakovlev popanda chikalata chowalola kuchita zimenezi

 3. 29 March, 2022

  Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba zinanso 5 za Mboni za Yehova kuphatikizapo nyumba ya bambo wina amene a Yakovlev ankaphunzira naye Baibulo. A Yakovlev anamangidwa n’kuwatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu

 4. 30 March, 2022

  Anakawatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu

 5. 20 June, 2022

  Mlandu unayamba kuzengedwa

Zokhudza M’baleyu

Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kuthandiza ndi kupatsa mphamvu atumiki ake okhulupirika pomwe nawonso akupitirizabe kumudalira.—Yesaya 40:31.