Pitani ku nkhani yake

M’bale Sergey Kuznetsov

6 JANUARY 2023
RUSSIA

“Ndikupitirizabe Kudalira Yehova”

“Ndikupitirizabe Kudalira Yehova”

Posachedwapa khoti la mumzinda wa Nevinnomyssk m’chigawo cha Stavropol lipereka chigamulo pa mlandu wokhudza M’bale Sergey Kuznetsov. Loya waboma sananenebe chilango chomwe akufuna kuti khoti lipereke kwa m’baleyu.

Zokhudza M’baleyu

Njira imene Yehova akusamalirira a Kuznetsov imalimbitsa chikhulupiriro chathu kuti Iye amaona ‘masautso athu onse’ komanso ‘adzatikweza m’mwamba ndi kutinyamula’ pamene tikukumana ndi mavuto.—Yesaya 63:9.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 21 November 2018

  Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba za a Mboni za Yehova kuphatikizapo nyumba ya a Kuznetsov

 2. 12 December 2019

  Anamutsegulira mlandu

 3. 18 June 2020

  Anamuika pamndandanda wa anthu ochita zinthu zoopsa

 4. 31 May 2022

  Anamuletsa kuti asatuluke m’dera la kwawo

 5. 7 September 2022

  Mlandu unayamba kuzengedwa