Pitani ku nkhani yake

M’bale Ilya Olenin ndi mkazi wake Natalya

2 AUGUST, 2022
RUSSIA

Ndikunyadira Kuti “Ndapanga Nawo Mbiri ya Gulu Lathu”

Ndikunyadira Kuti “Ndapanga Nawo Mbiri ya Gulu Lathu”

Pa 26 July 2022, Khoti la Mzinda wa Snezhinskiy m’Chigawo cha Chelyabinsk linapeza kuti M’bale Ilya Olenin ndi wolakwa. Loya woimira boma anapempha khotili kuti lipatse M’bale Olenin chilango chokakhala kundende zaka 6 ndi hafu. Koma m’malo mwake, khoti linagamula kuti m’baleyu alipire ndalama za ku United States zokwana madola 8,150.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 17 April, 2017

  Apolisi a FSB anasokoneza Mwambo wa Chikumbutso. Panthawiyi apolisiwa ananena kuti M’bale Olenin ali ndi mlandu “wogwira ntchito yaumishonale.” Komabe mlanduwo unatsekedwa

 2. 30 November, 2020

  Apolisi anakafufuza zinthu kunyumba kwa M’bale Olenin

 3. 28 September, 2021

  M’bale Olenin anamutsegulira mlandu

 4. 28 October, 2021

  Apolisi anabweranso kachiwiri kudzafufuza zinthu m’nyumba mwake. Pa nthawiyi anatenganso M’bale Olenin kuti akamufunse mafunso komanso anamuletsa kuti asapange ulendo uliwonse wochoka m’deralo

 5. 23 May, 2022

  Khoti linayamba kuzenga mlandu

Zokhudza M’baleyu

Tikusangalala kwambiri kuti M’bale Olenin komanso abale ndi alongo athu onse akuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu poyesetsa kuchitira umboni za Mulungu wathu wamkulu Yehova.—Yesaya 43:10.