Pitani ku nkhani yake

M’bale Danielyan ndi mkazi wake Nina

9 NOVEMBER 2022
RUSSIA

M’bale Andrey Danielyan Anagamulidwa Kuti Akakhale ku Ndende Zaka 6

M’bale Andrey Danielyan Anagamulidwa Kuti Akakhale ku Ndende Zaka 6

Pa 7 November 2022, khoti la mu mzinda wa Rubtsovskiy m’chigawo cha Altai linapeza olakwa M’bale Andrey Danielyan ndipo linagamula kuti akakhale ku ndende zaka 6. Ndipo anatengeredwa ku ndende nthawi yomweyo.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 25 May 2021

  M’bale Danielyan anamutsegulira mlandu pambuyo pofufuza komanso kumvetsera mwachinsisi zimene ankakambirana ndi anthu ena pa foni kwa miyezi ingapo.

 2. 26 May 2021

  Apolisi anakafufuza kunyumba kwa M’bale Danielyan. Pambuyo pake anatengedwa limodzi ndi mkazi wake kuti akawafunse mafunso. Ndipo M’bale Danielyan anamulamula kuti asayende kutuluka m’dzikolo.

 3. 13 July 2022

  Anamupeza ndi mlandu wotsogolera kagulu kochita zinthu zoopsa.

 4. 5 September 2022

  Mlandu unayamba kuzengedwa

 5. 7 November 2022

  Anamugamula kuti akakhale ku ndende kwa zaka 6

Zokhudza M’baleyu

Tikuyamikira chitsanzo cha M’bale Danielyan komanso abale ndi alongo ena amene akuyesetsa kukhalabe okhulupirika pamene tikuyembekezera ‘lonjezo la moyo umene ukubwerawo.’—1 Timoteyo 4:8

a M’bale Danielyan anafotokoza ndemanga zakezi atatsala pang’ono kuti alandile chigamulo.