Pitani ku nkhani yake

M’bale Aleksandr Shutov

12 SEPTEMBER, 2022
RUSSIA

M’bale Aleksandr Shutov Akupitirizabe Kudalira Yehova Kuti Azimutsogolera

M’bale Aleksandr Shutov Akupitirizabe Kudalira Yehova Kuti Azimutsogolera

Posachedwapa khoti la m’Boma la Lazo m’Chigawo cha Khabarovsk lipereka chigamulo chake pa mlandu wokhudza M’bale Aleksandr Shutov. Loya waboma sananene chilango chimene akufuna kuti khoti lipereke kwa m’baleyu.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 26 July, 2021

  Anawatsegulira mlandu

 2. 30 July, 2021

  Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba mwawo. Pambuyo pake anamanga a Shutov, n’kukawafunsa mafunso kenako anamasulidwa koma anawalamula kuti asatuluke m’dziko lawo.

 3. 3 August, 2021

  Analembedwa pa mndandanda wa anthu ochita zinthu zoopsa

 4. 28 April, 2022

  Mlandu unayamba kuzengedwa

Zokhudza M’baleyu

Pamene tikuzunzidwabe, panopa tiyeni tonse tipitirizebe kulimbitsa chikhulupiriro chathu komanso tikhale otsimikiza kuti ‘tidzakhulupirira kukoma mtima kosatha kwa Mulungu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.’—Salimo 52:8.