Pitani ku nkhani yake

Mlongo Irina Perefileva

1 MAY 2023
RUSSIA

“Mavuto Anga Ndi Osakhalitsa”

“Mavuto Anga Ndi Osakhalitsa”

Posachedwapa, Khoti la m’boma la Urupskiy lomwe lili ku Karachayevo-Circassian Republic lilengeza chigamulo chake pa mlandu wokhudza Mlongo Irina Perefileva. Loya woimira boma pamlanduwu akuyembekezereka kunena chilango chimene akufuna kuti chiperekedwe kwa mlongoyu.

Zokhudza Mlongoyu

Mofanana ndi Mlongo Irina, timatonthozedwa kudziwa kuti ngakhale mavuto amene tikukumana nawo angaoneke ngati ovuta kuwapirira, koma “ndi akanthawi ndiponso aang’ono” tikawayerekezera ndi madalitso amene Yehova wasungira atumiki ake okhulupirika m’tsogolomu.​—2 Akorinto 4:17.

Nthawi ndi Zochitika

 1. 9 January 2021

  Anachita chipikisheni m’nyumba yawo

 2. 22 November 2021

  Anamutsegulira mlandu

 3. 23 November 2021

  Anachitanso chipikisheni m’nyumba mwawo

 4. 29 November 2021

  Anauzidwa kuti ali ndi mlandu wochita zinthu ndi gulu loopsa

 5. 15 October 2022

  Analetsedwa kuchita zinthu zina

 6. 6 December 2022

  Mlandu unayamba kuzengedwa