Pitani ku nkhani yake

M’bale Anatoliy Senin

26 SEPTEMBER, 2022
RUSSIA

Kukhala pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova Kumathetsa Mantha

Kukhala pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova Kumathetsa Mantha

Khoti la mumzinda wa Kyzylskiy m’dziko la Tuva posachedwapa lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Anatoliy Senin. Loya wa boma sananene chilango chimene akufuna kuti m’baleyu apatsidwe.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 28 January, 2021

  Anamangidwa pambuyo poti apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba yake

 2. 30 January, 2021

  Anamasulidwa ndipo anauzidwa kuti akakhale pa ukaidi wosachoka panyumba

 3. 27 March, 2021

  Anamasulidwa pa ukaidi wosachoka panyumba koma analetsedwa kuti asatuluke m’dera limene amakhala

 4. 17 January, 2022

  Anamangidwa chifukwa chotsogolera ntchito za Mboni za Yehova

 5. 6 April, 2022

  Mlandu unayamba kuzengedwa

Zokhudza M’baleyu

Ndipotu tingalimbikitsidwe kwambiri tikaganizira mawu amene Yesu anauza ophunzira ake akuti: “Mitima yanu isavutike kapena kuchita mantha.”—Yohane 14:27.