Pitani ku nkhani yake

M’bale Sergey Kazakov

30 AUGUST, 2022
RUSSIA

‘Anapitirizabe Kudalira Yehova’

‘Anapitirizabe Kudalira Yehova’

Posachedwa khoti la Mzinda wa Bikinskiy m’Chigawo cha Khabarovsk lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Sergey Kazakov. Loya waboma sananene chilango chimene akufuna kuti khoti lipereke kwa m’baleyu.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 9 November, 2020

  Mlandu unatsegulidwa. M’bale Kazakov anazengedwa mlandu wotsogolera gulu lochita zinthu zoopsa

 2. 21 December, 2020

  Komiti yofufuza mlandu komanso apolisi a FSB anakafufuza zinthu m’nyumba zokwana 10 kuphatikizapo ya a Kazakov. Kenako apolisi anamanga a Kazakov n’kukawatsekera poyembekezera kuwazenga mlandu

 3. 23 December, 2020

  Anawatsekera m’ndende podikirira kuwazenga mlandu

 4. 4 June, 2021

  Anawatulutsa m’ndende ndi kuwaika pa ukaidi wosachoka panyumba

 5. 5 August, 2021

  Anawamasula pa ukaidi wosachoka panyumba

 6. 28 February, 2022

  Mlandu unayamba kuzengedwa. Panthawi yomvetsera mlandu, jaji anabwezanso mlanduwu kwa loya waboma chifukwa cholephera kutsatira ndondomeko yoyenera.

 7. 28 April, 2022

  Jaji anasintha zomwe ananena kuti mlandu ubwerere kwa loya waboma ndipo analamula kuti khoti lomwe linayamba kuzenga mlanduwu liyambirenso

 8. 14 June, 2022

  Mlandu unayambiranso kuzengedwa

Zokhudza M’baleyu

Pamene M’bale Kazakov akupitirizabe kudalira Yehova, ifenso tikugwirizana naye kuti mawu opezeka pa Salimo 31:14 ndi oona. Mawuwa amati: “Ine chikhulupiriro changa chili mwa inu Yehova. Ndipo ndikunena kuti: ‘Inu ndinu Mulungu wanga.’”