Pitani ku nkhani yake

5 OCTOBER, 2022
PORTUGAL

Buku la Mateyu Latulutsidwa mu Chikabuverdianu

Buku la Mateyu Latulutsidwa mu Chikabuverdianu

Pa 25 September 2022, M’bale Mário Pinto de Oliveira wa m’Komiti ya Nthambi ya Portugal, anatulutsa Baibulo la Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyu mu Chikabuverdianu. Buku la m’Baibuloli linatulutsidwa pamsonkhano wapadera womwe unajambulidwa ku nthambi ya Portugal mumzinda wa Lisbon. Ofalitsa 3,812 kuphatikizaponso ena amene anasonkhana m’Nyumba ya Ufumu ku Cape Verde ndi ku Portugal, anaonera msonkhanowu.

Chilankhulochi ndi Chipwitikizi chomwe chinapangidwa kuchoka ku Chikiliyo. Chikabuverdianu ndi chilankhulo chobadwira cha anthu ambiri omwe amakhala ku Cape Verde. Ofesi ya nthambi ya Portugal ndi imene imayang’anira ntchito yolalikira ku Cape Verde.

Ofesi yomasulira mabuku mu Chikabuverdianu yomwe ili ku Praia, Santiago, ku Cape Verde

Ponena za Baibulo latsopanoli, mmodzi wa ogwira ntchito yomasulira ananena kuti: “Ngakhale kuti Mabaibulo ena a mu Chikabuverdianu alipo, koma sapezekapezeka. Kwa anthu ambiri kukhala koyamba kuwerenga Mawu a Mulungu m’chilankhulo chawo.”

Womasulira winanso ananena kuti: “Baibuloli ndi losavuta kuwerenga, kulimvetsa komanso lili ndi mawu omwe timagwiritsa ntchito tsiku ndi tsiku polankhulana. Baibuloli ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova watipatsa ndipo lidzatithandiza kwambiri pa ntchito yolalikira. Panopa, tiziwafika anthu pamtima chifukwa sitizitayanso nthawi ndi kufotokozera matanthauzo a mawu ena.”

Kutulutsidwa kwa buku la Mateyu mu Chikabuverdianu ndi umboni wamphamvu woti Mulungu wathu wopanda tsankho adzaonetsetsa kuti anthu onse omwe amamufunafuna apeza Mawu ake.​—Machitidwe 10:34, 35.