NOVEMBER 8, 2019
PHILIPPINES
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Manila, Philippines
Masiku: 1 mpaka 3 November, 2019
Malo: Mall of Asia Arena ndiponso SMX Convention Center ku Manila, Philippines
Zinenero: Chingelezi, Chitagalogi
Chiwerengero cha Osonkhana: 26,245
Chiwerengero cha Obatizidwa: 145
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,397
Nthambi Zoitanidwa: Australasia, Central Europe, France, Indonesia, Italy, Japan, Kazakhstan, Madagascar, Malaysia, Myanmar, Papua New Guinea, Solomon Islands, South Africa, Sri Lanka, Taiwan, Thailand ndi United States
Zina Zomwe Zinachitika: A Rogelio Jolongbayan omwe ndi bwana wamkulu woona zokhudza makasitomala pamalo a zamalonda otchedwa Mall of Asia Arena, anati: “Pa makasitomala onse omwe takhala tikuchita nawo zinthu, gulu lanuli ndi la anthu aulemu komanso ochita zinthu mwadongosolo kwambiri. Tasangalala kwambiri kukhala nanu pamalo athuwa.”
A Nolasco Bathan omwe ali ndi udindo waukulu ku polisi ananena kuti: “Alendo onse ochokera kumayiko ena ankaima pamzere bwinobwino n’kumalowa pamalo athuwa popanda kukankhanakankhana. Zinthu zikamachitika mwadongosolo chonchi, ifeyo sitimafunikiranso kukhalapo!”
A Teofilo Labe Jr., omwe ndi wachiwiri kwa mkulu wa zachitetezo ku Manila Hotel, anapatsidwa ntchito yoyang’anira dongosolo la mmene alendo ochokera kumayiko ena azidzayendera akamapita kokaona malo. Ataona mmene abale ankayendetsera dongosololi, anati: “Ngati mabwana anga atandifunsa mmene mumayendetsera maulendo okaona malo, . . . ndidzawauza kuti munaposa wina aliyense. Gulu lanu limachita zinthu mwadongosolo kwambiri.”
Abale ndi alongo a ku Philippines akulandira alendo ku Beteli
Abale ndi alongo akugawira timapepala toitanira anthu kumsonkhano
Msonkhano usanayambe, abale 4 oimira ofesi ya nthambi akuchita msonkhano ndi atolankhani ndipo akuyankha mafunso awo
Anthu omwe anapezeka pamsonkhano ali kunja kwa malo a msonkhano
Alendo ochokera kumayiko ena akujambulitsa ndi abale ndi alongo a m’dzikoli
Abale ndi alongo akuimba nyimbo ya Ufumu pa nthawi ya msonkhano
Abale awiri akubatizidwa pa tsiku Loweruka
M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira, akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Loweruka
Alendo a mu utumiki wa nthawi zonse wapadera ali ndi M’bale Sanderson pa pulatifomu ndi patsogolo pake pa tsiku lomaliza la msonkhano
Abale ndi alongo akuvina gule wachikhalidwe cha ku Philippines wotchedwa Tinikling, pa zochitika zina zamadzulo

