Pitani ku nkhani yake

M’bale Hilarion Amores, mmodzi mwa anthu oyambirira kumasulira mabuku m’Chitagalog

30 AUGUST, 2022
PHILIPPINES

Anthu Akhala Akupindula ndi Nsanja ya Olonda ya Chitagalog kwa Zaka 75

Anthu Akhala Akupindula ndi Nsanja ya Olonda ya Chitagalog kwa Zaka 75

Pofika pa 1 September , 2022, zakwana zaka 75 kuchokera pamene Nsanja ya Olonda ya Chitagalog inayamba kusindikizidwa. Kungoyambira nthawi imeneyo, magazini ochuluka akhala akusindikizidwa kuchoka pa 600 kufika pa 1.2 miliyoni. Magaziniwa akupezekanso pazipangizo zamakono pa webusaiti yathu ya jw.org.

Uthenga wabwino unafika ku Philippines chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1908. Ofesi ya nthambi itakhazikitsidwa mu 1924, ntchito yolalikira inayamba kuyenda bwino. Mabuku a chingelezi ankagwiritsidwa ntchito kwambiri, komabe abale anaona kuti m’pofunika kukhala ndi mabuku a m’chiyankhulo cha Chitagalog.

Nkhondo Yachiwiri ya Padziko Lonse itangotha, M’bale Earl Stewart, Victor White, komanso M’bale Lorenzo Alpiche omwe anali amishonale, anafika ku Philippines pa 14 June , 1947. M’bale Stewart yemwe anali atangoikidwa kumene kukhala mtumiki wa nthambi, mofulumira anasankha abale oyenerera kuti ayambe kumasulira Nsanja ya Olonda mu Chitagalog. Pofika mu September chaka chomwecho, ofalitsa ankatha kugawira magazini a Nsanja ya Olonda a mitundu iwiri mwezi uliwonse.

Magazini osiyanasiyana a Nsanja ya Olonda a m’Chitagalog

Chakumayambiriro kwa ntchitoyi, ambiri mwa abale omwe ankagwira ntchito yomasulira, masana ankagwira ntchito zina kuti azikwanitsa kusamalira mabanja awo ndipo ntchito yomasulirayi ankaigwira usiku. M’bale Hilarion Amores yemwe ankagwira nawo ntchito yomasulirayi ananena kuti: “Tinkafunika kugwira ntchito mpaka 2 koloko m’bandakucha. Komabe tinkasangalala kwambiri chifukwa tinkasamalira abale mwauzimu.”

Panopa, ku Philippines kuli ofalitsa 97,443 omwe akutumikira mumipingo yokwana 1,126 ya Chitagalog. M’dzikoli muli anthu pafupifupi 76.5 miliyoni amene amalankhula Chitagalog ndipo padziko lonse pali ofalitsa oposa 115,000 omwe amalankhula chilankhulochi. Mabuku a Chitagalog akufalitsidwa m’mayiko ambiri ndipo amagwiritsidwa ntchito ndi ofalitsa omwe amalankhula chilankhulochi komanso anthu ena achidwi.

Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa kudzera m’gulu lake, akupereka chakudya chauzimu kwa anthu mamiliyoni m’zilankhulo zawo padziko lonse.—Mateyu 24:45, 46.