Pitani ku nkhani yake

30 MARCH, 2017
PERU

Kusefukira kwa Madzi Komanso Kugumuka kwa Nthaka ku Peru

Kusefukira kwa Madzi Komanso Kugumuka kwa Nthaka ku Peru

Mvula yamphamvu yachititsa kuti madzi asefukire komanso kuti nthaka igumuke m’madera ambiri m’dziko la Peru. Dzikoli lili ndi madera 25 ndipo dera limodzi lokha ndi limene silinakhudzidwe ndi kusefukira kwa madziku komabe malipoti akusonyeza kuti kusefukiraku kupitirirabe. Mvula imene yagwa m’dziko la Peru yawirikiza maulendo 10 poyerekezera ndi mvula yomwe imagwa nthawi zonse, kuyambira December mpaka March. A Mboni za Yehova akuthandiza anzawo amene akhudzidwa kusefukiraku komanso anthu ena omwe si Mboni.

Nyumba zoposa 530 za a Mboni za Yehova komanso malo awo olambirira (Nyumba za Ufumu) okwana 6 zawonongeka. Malipoti akusonyeza kuti m’tawuni ya Huarmey, yomwe ili pamtunda wa makilomita 288 kuchokera m’tawuni ya Lima, madzi osefukira anachititsa a Mboni ambiri kuthawira padenga la nyumba zawo.

Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dzikoli yapanga makomiti 8 opereka thandizo kwa a Mboni omwe akhudzidwa ndi ngoziyi, kuphatikiza omwe ali m’madera okwana 12 komwe boma lalengeza kuti ndi madera amene akhudzidwa kwambiri. Makomitiwa apereka kale chakudya chokwana matani 22 komanso madzi akumwa oposa malita 22, 000 kwa anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madziku. Chakudya chokwana matani 48 komanso madzi akumwa oposa malita 9,000 zitumizidwanso milungu yomwe ikubwerayi. A Mboni ambiri a m’dzikoli adzipereka kuti athandize pantchito yoyeretsa malo amene awonongeka komanso kukonza zinthu.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi limene limayendetsa ntchito yopereka thandizo kwa anthu okhudzidwa ndi ngozi zamwadzidzidzi kuchokera ku likulu lawo la padziko lonse. Iwo amagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo zothandizira ntchito ya Mboni yomwe ikuchitika padziko lonse.

Lankhulani ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Peru: Norman R. Cripps, +51-1-708-9000