Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 5, 2019
NIGERIA

Anthu “Anasangalala Kwambiri” Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Litatulutsidwa M’ziyankhulo Ziwiri za ku Nigeria

Anthu “Anasangalala Kwambiri” Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Litatulutsidwa M’ziyankhulo Ziwiri za ku Nigeria

Pa 12 January, 2019, abale athu ku Nigeria anali ndi msonkhano wapadera womwe unachitikira pa Malo a Msonkhano mumzinda wa Benin m’dzikolo. Pamsonkhanowu, m’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira, analengeza za kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’zinenero za Chiisoko ndi Chiyoruba. Anthu onse amene anamvetsera msonkhanowu anali 60,672. Kuonjezera pa anthu omwe anali pamalo a msonkhano mumzinda wa Benin, panali anthu enanso omwe anachita nawo msonkhanowu amene anasonkhana m’Nyumba za Ufumu 106 ndi m’Malo a Msonkhano 9 ku Nigeria, komanso m’madera ena a m’dziko la Benin lomwe ndi loyandikana ndi dziko la Nigeria.

M’bale Jackson limodzi ndi banja lina pa Malo a Msonkhano mumzinda wa Benin ku Nigeria

M’bale Gad Edia wa ku ofesi ya nthambi ya Nigeria ananena kuti: “Zinatenga zaka zitatu ndi miyezi iwiri kuti ntchito yomasulira Baibulo la Chiisoko imalizidwe ndipo kumasulira Baibulo la Chiyoruba kunatenga zaka zitatu ndi miyezi itatu.” M’baleyu ananenanso kuti: “Ku Nigeria a Mboni oposa 5,000 amalankhula Chiisoko ndipo ena oposa 50,000 amalankhula komanso kuwerenga Chiyoruba. Pofotokoza mmene abale anamvera atangolandira Baibulo lawo lokonzedwanso, munthu wina ananena kuti anthu ‘anasangalala kwambiri.’ Choncho tinganene motsimikiza kuti khama lomwe linalipo pomasulira Mabaibulowa silinapite pachabe.”

Pofika pano, a Mboni za Yehova amasulira Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu kapena mbali zake zina m’zinenero 179.

Tikusangalala kwambiri kuti tsopano abale athu aziwerenga komanso kuphunzira Baibulo mosavuta m’zinenerozi.—2 Timoteyo 3:17.