Pitani ku nkhani yake

MAY 28, 2019
MOZAMBIQUE

Mphepo Yamkuntho ya Kenneth Inaomba Mwamphamvu Kumpoto kwa Mozambique

Mphepo Yamkuntho ya Kenneth Inaomba Mwamphamvu Kumpoto kwa Mozambique

Pa 25 April, 2019, Mphepo Yamkuntho ya Kenneth inaononga kumpoto kwa Mozambique. Mphepo yamkunthoyi ndi yachiwiri kuomba m’dzikoli pambuyo pa Mphepo Yamkuntho ya Idai yomwe inaononga zinthu m’madera ambiri m’mwezi wa March. Mphepo ya Kenneth inachititsa kuti madzi asefukire kwambiri komanso nthaka inakokoloka n’kuwononga nyumba za anthu, kukokolola misewu, komanso inapitiriza kuononga zinthu zomwe zinali kale zoonongeka.

M’chigawo cha Cabo Delgado muli ofalitsa 300 koma palibe amene anavulala kapena kufa ndi mphepoyi. Komabe nyumba 9 za abale zinagweratu ndipo 16 zinaonongeka. Komanso, Nyumba ya Ufumu imodzi inagweratu ndipo zitatu zinaonongeka. Woyang’anira dera, woimira Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga, ndiponso abale awiri ochokera kuofesi yomasulira mabuku anapita kukayendera mipingo yonse yomwe inakhudzidwa ndi ngoziyi komanso analimbikitsa abale ndi alongo.

Tikupempherera abale athu pamene akupitiriza kudalira Yehova kuti awalimbitse komanso kuwathandiza “pa nthawi ya masautso.”—Salimo 46:1.