Pitani ku nkhani yake

6 OCTOBER, 2022
MOZAMBIQUE

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa m’Chisena

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa m’Chisena

Pa 2 October 2022, M’bale David Amorim wa m’Komiti ya Nthambi ya Mozambique, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika mu Chisena. a Baibuloli linatulutsidwa pamsonkhano wochita kujambulidwa ndipo ofalitsa ambiri anaonera pulogalamu ya msonkhanowu ali m’Nyumba za Ufumu za m’madera awo. Msonkhanowu unawulutsidwanso pa TV ya boma komanso pa masiteshoni a wailesi.okwana 14.

Chisena chimalankhulidwa m’zigawo 4 za ku Mozambique. Zigawo zake ndi Manica, Sofala, Tete, ndi Zambezia. Chisena chimalankhulidwanso m’madera ena a ku Malawi.

Ofesi yomasulira mabuku ya Chisena yomwe ili ku Beira m’dziko la Mozambique

Kameneka ndi koyamba kuti a Mboni za Yehova amasulire Baibulo la Dziko Latsopano lonse lathunthu mu chimodzi mwa zilankhulo zakale za m’dzikolo. Baibuloli lisanatulutsidwe, zigawo zina za Baibulo zinkapezeka m’Chisena koma zinali zodula komanso zinali ndi mawu achikale omwe anthu anasiya kuwagwiritsa ntchito.

Tikusangalala limodzi ndi abale ndi alongo athu olankhula Chisena chifukwa cha madalitso apaderawa ochokera kwa Yehova.—Miyambo 10:22.

a Baibuloli likupezeka la pa zipangizo zamakono komanso lochita kusindikiza.