JUNE 20, 2019
MEXICO
Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Monterrey, Mexico
Masiku: 7 mpaka 9 June, 2019
Malo: BBVA Bancomer Stadium ku Monterrey, Mexico
Zinenero: Chingelezi, Chinenero Chamanja cha ku Mexico, Chisipanishi
Chiwerengero cha Malo Omwe Analumikizidwa: Malo 38 a m’mayiko 6 osiyanasiyana (Costa Rica, Guatemala, Honduras, Mexico, Nicaragua, ndi Panama)
Chiwerengero cha Osonkhana: 39,099
Chiwerengero cha Obatizidwa: 393
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 4,682
Nthambi Zoitanidwa: Argentina, Brazil, Colombia, France, Italy, Japan, the Netherlands, Paraguay, Peru, Spain, United States
Zina Zomwe Zinachitika: A Roberto Valero omwe ndi nthumwi ya meya wa mzinda wa Guadalupe, anapita ku malo a msonkhano Loweruka. Mwa zina, iwo anati: “Chimodzi mwa zolinga zikuluzikulu za boma lathu ndi kuonetsetsa kuti anthu akukhala motetezeka komanso mwamtendere. Ndipo inuyo a Mboni za Yehova mwatithandiza kwambiri kukwaniritsa cholinga chimenechi chifukwa ndinu nzika zabwino. Mzinda wonsewu umadziwa bwino zimenezi.”
Abale ndi alongo akulandira alendo pabwalo la ndege la Monterrey International Airport
Alendo ochokera kumayiko ena akufika pamalo a msonkhano ndipo phiri lokongola kwambiri la Mount Silla likuoneka kutsogolo
M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Lachisanu
Munthu akubatizidwa Loweruka mu limodzi mwa madamu 4 obatizira omwe anagwiritsa ntchito pamsonkhanowu
Alendo ochokera kumayiko ena akumvetsera mwachidwi nkhani za pamsonkhano
Alendo omwe ali muutumiki wa nthawi zonse wapadera akubayibitsa anthu pa tsiku lomaliza la msonkhanowu
Banja lochokera mumzinda wa Apodaca ku Mexico lanyamula nsalu yomwe alembapo kuti, ‘Timakukondani’
Mlendo wochokera kudziko lina akulalikira ku Monterrey ndi mlongo wa ku Mexico
Alendo ochokera kumayiko ena akusangalala ndi gule wa kumpoto kwa Mexico wotchedwa Polka Norteña
Alongo akuvina gule wachikhalidwe wa ku Jalisco, Mexico