APRIL 2, 2019
KAZAKHSTAN
A Mboni za Yehova ku Kazakhstan Anaitana Anthu Kuti Akaone Nyumba za Ufumu
Kuyambira pa 11 May mpaka pa 10 November, 2018, a Mboni za Yehova ku Kazakhstan anaitana anthu kuti akaone Nyumba za Ufumu m’mizinda yosiyanasiyana 7 ya m’dzikolo. Zimenezi zinapereka mwayi kwa akuluakulu a boma, atolankhani, mapulofesa komanso anthu ena kuti adziwe zambiri zokhudza a Mboni za Yehova. Anthu onse omwe anapezekako anali oposa 1,500.
Madera omwe anthu anapita kukaona Nyumba za Ufumu: (1) Öskemen, (2) Qaraghandy, (3) Qostanay, (4) Semey, (5) Shymkent, (6) Taldyqorghan, ndi (7) Taraz.
Anthu anaitanidwa kukaona Nyumba za Ufumu za m’mizinda ya Öskemen, Qaraghandy, Qostanay, Semey, Shymkent, Taldyqorghan, ndi Taraz. Iwo anasangalala kuona matchati ndi zithunzi zofotokoza mbiri ya zomwe a Mboni za Yehova akhala akuchita ku Kazakhstan kuyambira mu 1892. Zithunzizi zinkafotokozanso zomwe a Mboni za Yehova akwanitsa kuchita posachedwapa monga kutulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chikazaki mu 2014.
M’bale Bekzat Smagulov yemwe amagwira ntchito mu Dipatimenti ya Zamalamulo komanso mu Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ku ofesi ya nthambi ya Kazakhstan anafotokoza zinthu zosangalatsa zomwe zinachitika pa nthawi yomwe anthu ankaona Nyumba za Ufumu. Iwo anati: “Anthu anayamikira zimene anaona ndipo zinawathandiza kudziwa zoona zokhudza a Mbonife. Ena mwa alendowa anali akuluakulu ochokera ku Dipatimenti Yoona za Zipembedzo ndi atolankhani ochokera ku bungwe lina lofalitsa nkhani mumzinda wa Öskemen, nyuzipepala ya Rudnyi Altai komanso ya Semei Vesti.”
Ku Nyumba ya Ufumu ya mumzinda wa Taldyqorghan womwe ndi likulu la m’chigawo cha Almaty, abale analandira mkulu wa Dipatimenti Yoona za Zipembedzo m’chigawo cha Almaty komanso akuluakulu ena awiri a m’dipatimentiyi. Kunabweranso mkonzi wamkulu wa nyuzipepala ya Zhetysu Dialog, yemwe kenako analemba nkhani kuchokera pa mafunso omwe anafunsa abale ndi alongo ena omwe anali kumalowo.
Kuonjezera pamenepo, abale ndi alongo athu anagawira Mabaibulo a Dziko Latsopano oposa 560 a Chikazaki komanso a Chirasha, zomwe ndi zilankhulo zikuluzikulu ku Kazakhstan. Tikuyamikira chifukwa cha dongosolo limeneli lomwe lachititsa kuti Yehova alemekezeke komanso kuti anthu aone ‘ntchito zathu zabwino.’—Mateyu 5:16.
Ku Qaraghandy, Mlongo Saniya Akhmetzhanova akufotokozera banja la vuto losamva m’chinenero chamanja zokhudza ntchito yathu yophunzitsa Baibulo anthu a vuto losamva.
Ana awiri akuonera vidiyo yakuti Tetezani Ana Anu ya Chirasha m’Nyumba ya Ufumu ku Qaraghandy.
M’bale Lev Gladyshev akufotokozera akuluakulu ena a mumzinda wa Qaraghandy zokhudza mbiri ya Mboni za Yehova ku Kazakhstan. Ena mwa akuluakuluwa anali a Kudaibergen Beksultanov omwe ndi mlembi wa nyumba ya malamulo ya mumzindawu, a Nikolay Sarsenbayev omwe ndi katswiri m’dipatimenti younika mmene zinthu zilili pa nkhani za zipembedzo (Department of Analysis of the Religious Situation), komanso a Nurlan Bikenov omwe ndi mkulu wa dipatimenti yoona za chipembedzo m’chigawo cha Qaraghandy.
Mlongo Aisha Yakovleva akufotokozera banja lina zokhudza mbali zosiyanasiyana za JW Library® ku Taldyqorghan.
M’bale Aleksey Alyoshin akuonetsa alendo amene anabwera kudzaona Nyumba ya Ufumu ya ku Taraz mmene dzina la Mulungu lakhala likupezekera m’mabuku komanso pa zinthu zakale zopanga pamanja..
Ku Nyumba ya Ufumu ya ku Öskemen, m’bale Sergey Petkevich wanyamula Nsanja ya Olonda yakale ya Chirasha pamene akufotokoza mbiri ya Mboni za Yehova ku Kazakhstan. Ena mwa alendo omwe anali ku malowa anali a Sergey Lebedev omwe ndi mkulu wa gulu la Edinstvo.
M’bale Georgiy Pismenoy (kumanja) akulankhula ndi neba wake yemwe anakaona Nyumba ya Ufumu ku Qostanay. Anthu anaonera vidiyo ya mlandu womwe unazengedwa mu 1982 wokhudza abale atatu ndi mlongo mmodzi ochokera ku Qostanay omwe anawapeza olakwa chifukwa chopezeka, kupanga komanso kugawira mabuku athu omwe anali oletsedwa pa nthawiyo. M’bale Pismenoy anali m’modzi mwa abale atatu omwe anagamulidwa kuti akagwire ukaidi wakalavulagaga kwa zaka ziwiri ndi hafu. Iye anafotokozeranso anthu zomwe anakumana nazo ali m’ndende.
Ku Nyumba ya Ufumu ya ku Shymkent, alendo analandiridwa ndi oimba omwe ankaimba ndi zida zosiyanasiyana, kuphatikizapo zida zotchedwa dombra za ku Kazakhstan (zomwe akuimba anthu omwe avala zipewa).
Abale ndi alongo omwe anadzipereka kuthandiza nawo ntchito zosiyanasiyana pa nthawi yoona Nyumba ya Ufumu ku Qaraghandy.