Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Maofesi a nsanjika 9 omwe akukonzedwanso ku Bologna, Italy

OCTOBER 23, 2019
ITALY

Ntchito Yomanga Nyumba Zatsopano za Beteli Ili Mkati ku Italy

Ntchito Yomanga Nyumba Zatsopano za Beteli Ili Mkati ku Italy

Nyumba yomwe panopa muli Dipatimenti Yomasulira Mabuku ku Imola

Ofesi ya nthambi ku Italy ikusamutsidwa kuchoka ku Rome kupita m’mizinda ya Bologna ndi Imola. Mzinda wa Bologna uli pamtunda wa makilomita pafupifupi 370 kumpoto kwa Rome pamene mzinda wa Imola uli pamtunda wa makilomita pafupifupi 48 kuchokera ku Bologna. Ntchito yokonzanso nyumba ya nsanjika 9 ku Bologna yomwe idzakhale maofesi a nthambiyi yayambika kale. Pofika mu 2018, atumiki a pa Beteli okwana 60 omwe amagwira ntchito yomasulira komanso ntchito zina, akhala akugwirira ntchito zawo ku Imola m’nyumba yatsopano yomwe inakonzedwanso.

Pofuna kuti abale ndi alongo otumikira ku Beteli omwe akusamukira ku Bologna asamavutike kupeza nyumba zokhalamo, pakumangidwa nyumba ya nsanjika 7 ndipo pansi pake pali malo oimika magalimoto okhala ndi mbali zitatu. Nyumbayi ili pamtunda wa pafupifupi kilomita imodzi ndi hafu kuchokera pamene pali maofesi. Pamalowa padzamangidwanso nyumba zina.

Chithunzi chojambula pakompyuta chosonyeza mmene nyumba yogona ya nsanjika 7 imene ikumangidwa panopa idzaonekere

Mu 1948, a Mboni za Yehova anagula nyumba ku Rome zomwe zinakhala ofesi yawo yanthambi yoyamba ndipo n’kumene anayamba kugwirira ntchito zawo atasamuka ku Milan. Kungoyambira nthawi imeneyi, chiwerengero cha ofalitsa ku Italy chinayamba kukwera kwambiri. Mkatikati mwa zaka za m’ma 1940, m’dzikoli munali ofalitsa osakwana 200. Koma pano kuli ofalitsa oposa 250,000, chomwe ndi chiwerengero chapamwamba kwambiri pa nthambi zonse za ku Europe. Pamene chiwerengero cha ofalitsa chinkakula, nachonso chiwerengero cha anthu otumikira pa Beteli ndi nyumba zina za Nthambi chinkakulanso. Pa nthawi yomwe ziwerengerozi zinakwera mu 2006, ofesi ya nthambi inawonjezera nyumba zosiyanasiyana 99. Ntchito yosamuka ikadzatha, chiwerengero cha anthu otumikira pa Beteli chidzachepetsedwa komanso pa Beteli padzakhala nyumba 5 zokha.

Tikupemphera kuti Yehova apitirize kudalitsa ntchitoyi komanso kuti nyumba zatsopanozi zithandize pa ntchito yomwe ikuchitika m’dziko la Italy, lomwe ndi m’munda momwe “mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.”—Yohane 4:35.