Pitani ku nkhani yake

Nyumba ya Ufumu imene abale ndi alongo athu awomberedwa. Anthu a ku Hamburg ndiponso akuluakulu a boma anaika maluwa pakhomo lolowera posonyeza chisoni chawo

20 MARCH 2023
GERMANY

Munthu Wawombera Abale ndi Alongo ku Hamburg, Germany

Munthu Wawombera Abale ndi Alongo ku Hamburg, Germany

Monga mmene nkhani ina yapawebusaitiyi inanenera, pa 9 March 2023, munthu wina anawombera abale ndi alongo amumpingo wa Hamburg-Winterhude misonkhano ya mkati mwa mlungu itangotha. Munthuyo anasiya kuwomberako apolisi atafika pa Nyumba ya Ufumu koma anali atapha komanso kuvulaza abale ndi alongo ambiri. Kenako anadzipha. A Mboni za Yehova kumeneko komanso padziko lonse akuyamikira kwambiri chikondi, kukoma mtima komanso chifundo chimene akuluakulu a boma, mabungwe ndiponso anthu ena padziko lonse awasonyeza pa nthawi yovutayi.

Mmene Zimenezi Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • N’zachisoni kuti abale 4, alongo awiri ndiponso mwana wosabadwa wa mlongo wina anaphedwa

  • Abale awiri ndi alongo 7 anavulala

Ntchito Yothandiza Abale ndi Alongo

  • Abale oimira ofesi ya nthambi ya Central Europe, oyang’anira madera awiri komanso akulu am’deralo akuthandiza abale ndi alongo powalimbikitsa

Monga gulu logwirizana la abale ndi alongo padziko lonse, tikupempherera onse amene akhudzidwa ndi chiwembuchi. Yehova ndi “malo achitetezo pa tsiku la nsautso” ndipo atithandiza kupirira mavuto amene tikukumana nawo masiku ano pamene tikupitiriza kumulambira mwamtendere.​—Nahumu 1:7.