Pitani ku nkhani yake

21 MARCH 2023
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Webusaiti ya JW.ORG Yakwanitsa Zaka 10​—Gawo 3

Kuthandiza Ntchito Yolalikira

Webusaiti ya JW.ORG Yakwanitsa Zaka 10​—Gawo 3

Nkhani zapitazi zasonyeza mmene webusaiti ya jw.org yathandizira potulutsa mabuku, mavidiyo ndi zinthu zina zapazipangizo zamakono komanso kufalitsa nkhani zolondola zokhudza abale ndi alongo athu padziko lonse. Munkhani ino yomwe ndi yomaliza pamituyi, tiona mmene webusaiti ya jw.org yagwiritsidwira ntchito pothandiza ntchito yolalikira padziko lonse.

Zilankhulo: Webusaiti ya jw.org itakonzedwanso mu August 2012, tsamba loyamba linkapezeka m’zilankhulo 139. Pofika mu August 2014, chaka chimene tinagwira ntchito yogawira kapepala kodziwitsa anthu za webusaiti yathu, chiwerengero cha zilankhulozi chinapitirira 500. N’zochititsa chidwi kuti pa chiwerengerochi panalinso zinenero 22 zamanja. Masiku ano, pawebusaitiyi pali zilankhulo zoposa 1,070, kuphatikizapo zinenero zamanja zoposa 100.

Nkhani za pa Nthawi Yake: Mu October 2019, tsamba loyamba la webusaiti ya jw.org linakonzedwanso kuti pamwamba pake pazikhala nkhani ndi chithunzi chachikulu komanso nkhani zina zitatu pansi pake n’cholinga choti zizikopa chidwi cha anthu omwe amalowa pawebusaitiyi. Zimenezi zimathandiza kuti anthu asamavutike kupeza nkhani zapawebusaitiyi zokhudza ntchito yathu yolalikira. Kenako Dipatimenti Yolemba Nkhani ndi Dipatimenti ya Zithunzi inakonza ndondomeko yofulumirirako yopangira nkhani zimenezi ndi zithunzi pofuna kuonetsetsa kuti tsamba loyamba likumakhala ndi zinthu pa nthawi yake ndiponso nkhani zatsopano zongochitika kumene. Mwachitsanzo, tsamba loyamba lili ndi nkhani zokhudza mliri wa COVID-19 womwe wakhudza anthu padziko lonse komanso nkhondo yomwe ikuchitika ku Russia ndi ku Ukraine ndiponso mavuto amene anthu othawa kwawo akukumana nawo.

Kudziwitsa Anthu Zokhudza Ifeyo pa Intaneti: Webusaiti ya jw.org imathandiza anthu amene ali ndi mtima wabwino kupeza nkhani zolondola zokhudza gulu lathu ndiponso ntchito yomwe timagwira. Imathandizanso anthu kudziwa zimene angachite kuti alankhule ndi a Mboni za Yehova ngati akufuna zambiri. Mayi wina yemwe ali ndi vuto losamva ankaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ali kupulayimale koma anasiya chifukwa anasamuka. Iye ankafuna kupitiriza kuphunzira Baibulo koma panalibe wa Mboni aliyense amene ankabwera kunyumba kwake. Kenako anakumbukira za webusaiti ya jw.org ndipo pogwiritsa ntchito fomu yapawebusaitiyi, anapempha kuti aziphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Patangopita masiku ochepa, apainiya apadera awiri anagogoda pakhomo pa mayiyu. Anayambiranso kuphunzira Baibulo komanso anayamba kusonkhana ndi a Mboni za Yehova. Panopa anabatizidwa ndipo akuphunzitsa Baibulo ana ake atatu. Iye anati: “Ndimathokoza Yehova kuti tili ndi webusaitiyi chifukwa ndikanapanda kulemba fomuyi ndikanafunika kudikira mpaka nditakumana ndi wa Mboni za Yehova.”

Pamene ntchito yolalikira ikukulirakulirabe, n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti gulu la Yehova likupitiriza kupereka zinthu zofunikira pothandiza anthu ambiri achidwi.​—Yesaya 60:22.

  • Mavidiyo amene anthu amapanga dawunilodi mwezi uliwonse

  • Anthu amene amalowa pawebusaitiyi tsiku lililonse

  • Kutulutsidwa kwa chizindikiro chovomerezeka cha jw.org, March 2013

  • Kupezeka kwa webusaitiyi m’zinenero zamanja, July 2014

  • Kukonzedwanso kwa tsamba loyamba kuti lizikopa chidwi anthu ambiri, October 2019

  • Kutulutsidwa kwa buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, January 2022