Pitani ku nkhani yake

Mkuntho wa Fiona womwe unabwera ndi mphepo komanso mvula yamphamvu, unawononga kwambiri

26 SEPTEMBER, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mkuntho wa Fiona Unawononga ku Caribbean

Mkuntho wa Fiona Unawononga ku Caribbean

Pa 18 September 2022, mphepo yamkuntho ya Fiona inadutsa ku Puerto Rico komanso kuzilumba zoyandikana ndi dzikoli. Mphepoyi inkathamanga pamtunda wa makilomita 160 pa ola limodzi ndipo madzi a mvula analowa pansi kufika masentimita 75. Mkunthowu unawononga misewu, mabuliji komanso zipangizo zamagetsi. Akuluakulu aboma akukumana ndi mavuto aakulu akamakapereka chakudya, madzi komanso mankhwala kwa anthu okhudzidwa chifukwa cha kuwonongeka kwa misewu ndi mabuliji.

Mmene zakhudzira abale ndi alongo athu

Puerto Rico, Saint Kitts and Nevis komanso Turks and Caicos

 • Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa pangoziyi

 • Ofalitsa 4 anavulala pang’ono

 • Ofalitsa 75 anasamuka m’nyumba zawo

 • Nyumba 140 zinawonongeka pang’ono

 • Nyumba 18 zinawonongeka kwambiri

 • Nyumba imodzi inawonongekeratu

Ku Dominican Republic

 • Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa pangoziyi

 • Ofalitsa 58 anasamuka m’nyumba zawo

 • Nyumba 57 zinawonongeka pang’ono

 • Nyumba 26 zinawonongeka kwambiri

 • Nyumba ziwiri zinawonongekeratu

 • Nyumba za Ufumu ziwiri zinaonongeka pang’ono

 • Nyumba za Ufumu ziwiri zinaonongeka kwambiri

Ku Guadeloupe ndi ku Martinique

 • Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa pangoziyi

 • Ofalitsa 16 anasamuka m’nyumba zawo

 • Nyumba 43 zinawonongeka pang’ono

 • Nyumba ziwiri zinawonongeka kwambiri

 • Nyumba za Ufumu 13 zinaonongeka pang’ono

Ntchito Yopereka Chithandizo

 • Oyang’anira madera komanso akulu akumadera okhudzidwawa, akuchititsa maulendo aubusa kwa mabanja amene anakhudzidwa ndi ngoziyi komanso kuwapatsa chithandizo

 • Ntchito yopereka chakudya, madzi, mankhwala komanso yokonza nyumba za abale zimene zinawonongeka ili mkati.

 • Ntchito yopereka chithandizoyi ikugwiridwa motsatira njira zonse zodzitetezera ku COVID-19

Tikudziwa kuti abale ndi alongo amene anakhudzidwa ndi ngoziyi atonthozedwa chifukwa cha chikondi chachikulu chimene abale ndi alongo amasonyezana.—Machitidwe 11:29.