JULY 26, 2019
DENMARK

Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Copenhagen, Denmark

Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Copenhagen, Denmark
  • Masiku: 19 mpaka 21 July, 2019

  • Malo: Brøndby Stadium ndi Brøndby Hallen, Copenhagen, Denmark

  • Zinenero: Chidanishi, Chinenero Chamanja cha ku Denmark, Chingelezi, Chiayisilandi, Chinenero Chamanja cha ku Norway, Chinenero Chamanja cha ku Sweden

  • Chiwerengero cha Osonkhana: 26,409

  • Chiwerengero cha Obatizidwa: 141

  • Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 7,000

  • Nthambi Zoitanidwa: Australasia, Brazil, Central America, Central Europe, Colombia, Dominican Republic, Finland, Georgia, India, Japan, Poland, ndi United States

  • Zina Zomwe Zinachitika: A Christian Tidemand Andersen omwe amayendetsa dongosolo la zochitika zosiyanasiyana pa sitediyamu ya Brøndby, anati: “Tinayamba kukonzekera Msonkhano Wamayiko wa Mboni za Yehova chaka chimodzi ndi hafu zapitazo, ndipo kungoyambira tsiku loyamba pakhala pali zokambirana zabwino kwambiri pakati pa ife ndi a Mboni. Mbali zonse ziwiri zinkalemekezana ndipo zinkadziwa bwino mavuto omwe angakhalepo pokonza dongosolo la msonkhano waukulu ngati umenewu. Zimenezi zinachititsa kuti zokonzekera zonse ziyende bwino kwambiri. Si kawirikawiri kukumana ndi gulu lomwe limachita zinthu mwadongosolo komanso lomwe limaganizira mfundo zonse zimene ziyenera kutsatidwa. Pa masiku omwe msonkhanowu unkachitika, zinali zosangalatsa kwambiri kuona anthu onse omwe anadzipereka amene anathandiza komanso kugwira ntchito kuyambira m’mawa mpaka usiku ndipo anagwira ntchito ndi mtima wodzipereka komanso nkhope zawo zinali zosangalala. Zinali zosangalatsa kwambiri kuthandiza nawo poyendetsa dongosolo la msonkhanowu ndipo tikuthokoza kwambiri Komiti ya Msonkhano ndi anthu onse ongodzipereka chifukwa sitinavutike pochita nawo zinthu. Tikukhulupirira kuti nthawi ina tidzakuwonaninso limodzi ndi alendo anu kuno ku Brøndby Stadium.”

 

Atumiki a pabeteli avala tizingwe tachikasu m’khosi ndipo akubayibitsa komanso kulandira mosangalala alendo omwe akudzaona Beteli

Ana limodzi ndi makolo awo akulandira alendo kumsonkhano wokonzekera utumiki wakumunda

Abale ndi alongo akufika pasitediyamu ya Brøndby kudzachita msonkhano

Alendo ochokera kumayiko ena akujambulitsa atavala zovala zakwawo

Alongo oyankhula Chiayisilandi akugwetsa misozi yachisangalalo atalandira Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la chinenero cha Chiayisilandi lomwe langotulutsidwa kumene

M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Lachisanu

Omwe akuyembekezera kubatizidwa akumvetsera nkhani m’bwalo la sitediyamu atakhala kutsogolo kwa pulatifomu

Ena mwa abale ndi alongo 141 atsopano akubatizidwa

Amishonale komanso anthu ena omwe ali mu utumiki wanthawi zonse wapadera akubayibitsa abale ndi alongo musitediyamu

Abale akupanga sewero lomwe linafotokoza nkhani yokhudza mbiri ya choonadi ku Denmark, Faroe Islands, Greenland, ndi Iceland