AUGUST 30, 2018
CANADA
Khoti Lalikulu Kwambiri ku Canada Lagamula Kuti Makhoti Sayenera Kulowerera Dongosolo Lochotsa Munthu Mumpingo
Pa 31 May, 2018, pozenga mlandu wa pakati pa Mpingo wa Mboni za Yehova wa Highwood (Komiti Yoweruza) ndi a Wall, Khoti Lalikulu Kwambiri la ku Canada linapanga chigamulo chomwe anthu onse anagwirizana nacho. Khotili linagamula kuti “magulu a zipembedzo ali ndi ufulu wovomereza amene angakhale membala wawo komanso kukhazikitsa malamulo oyendetsera chipembedzo chawo,” zomwe zikusonyeza kuti makhoti sayenera kulowerera dongosolo lochotsa munthu mumpingo.
Khoti Lalikulu Kwambiri ku Canada (nyumba yomwe ikuoneka chakumanzere) mumzinda wa Ottawa.
Khotili linanena kuti dongosolo lomwe a Mboni amayendera akamaweruza munthu yemwe wachita tchimo lalikulu “si lankhanza koma cholinga chake n’kuthandiza munthuyo kuti abwererenso mumpingo,” ndipo linagamula kuti makhoti sangalowerere nkhani zampingo zomwe sizikuwakhudza.
Pofotokoza zifukwa zomwe anaperekera chigamulochi, woweruza wina wa Khoti Lalikulu Kwambiri dzina lake Malcolm Rowe, analankhula m’malo mwa oweruza 9 omwe anapanga chigamulocho kuti: “Malamulo a gulu lachipembedzo angaphatikizepo mmene amatanthauzira ziphunzitso ngati mmene zakhalira ndi mlandu umenewu. Makhoti alibe mphamvu kapena udindo woweruza nkhani zokhudzana ndi ziphunzitso za chipembedzo.”
A Philip Brumley omwe ndi loya woimira Mboni za Yehova anati: “Chigamulo cha Khoti Lalikulu Kwambiri ku Canada chikugwirizana ndi zimene makhoti aakulu ku Argentina, Brazil, Hungary, Ireland, Italy, Peru, Poland, ndi United States anagamula, zoti tili ndi ufulu wotsatira zimene Malemba amanena pa nkhani yosankha amene ali woyenerera kukhala wa Mboni za Yehova.”—1 Akorinto 5:11; 2 Yohane 9-11.