JULY 26, 2019
CANADA
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Toronto, Canada
Masiku: 19 mpaka 21 July, 2019
Malo: Exhibition Place, Toronto, Ontario, Canada
Zinenero: Chingelezi, Chipwitikizi, Chisipanishi
Chiwerengero cha Osonkhana: 46,183
Chiwerengero cha Obatizidwa: 317
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,000
Nthambi Zoitanidwa: Brazil, Britain, Central America, Finland, India, Japan, Korea, Philippines, Ukraine, ndi United States
Zina Zomwe Zinachitika: Mayi Laura Purdy omwe ndi mkulu wa zamalonda komanso zochitika pa Exhibition Place, anati: “Zonse zimene komiti ya msonkhano [ya Mboni za Yehova] inanena zokhudza zinthu zabwino zomwe adzachite pamalowa, zachitikadi. Patokha tinachita kafukufuku pang’ono komanso tinalankhula ndi anthu a kumalo ena komwe a Mboni anachitiranso misonkhano yawo, ndipo tinapeza kuti nakonso kunachitika zofanana ndi zimene zikuchitika kuno.” Mayi Purdy ananenanso kuti: “Anthu pamsonkhanowu anali aubwenzi. Ndikufuna kulimbikitsa anthu ena omwe ali ndi malo ochitirako zinthu zosiyanasiyana kuti azilandira a Mboni m’mizinda yawo akafuna kuchita misonkhano.”
Abale ndi alongo akulandira alendo pabwalo la ndege ku Toronto
Alendo ochokera kumayiko ena akusangalala kulowera limodzi muutumiki ndi anzawo a ku Toronto
Abale ndi alongo omwe amatumikira ku Beteli akuimbira nyimbo alendo omwe anapita kukaona ofesi ya nthambi ya ku Canada
M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Lachisanu
Mmodzi mwa abale ndi alongo 317 atsopano akubatizidwa pa tsiku Loweruka
Abale ndi alongo akulemba notsi pamene akumvetsera msonkhano
Amishonale komanso abale ndi alongo ena omwe ali muutumiki wanthawi zonse akuyenda kutsogolo kwa malo a msonkhano ndipo anthu akuomba m’manja posonyeza kuyamikira utumiki wawo
Alongo 5 akubwereza zomwe zinaulutsidwa pawailesi ya CKCX m’zaka za m’ma 1920 yomwe pa nthawiyo inali ku Toronto, Canada. Pofika mu 1926, Ophunzira Baibulo (lomwe linali dzina la a Mboni za Yehova pa nthawiyo) anali ndi masiteshoni a wailesi m’mizinda 4 ya ku Canada, ndipo zimenezi ndi zosaiwalika m’mbiri ya choonadi ku Canada
M’bale wa ku Canada akutsogolera gulu la achinyamata poimba nyimbo. Imeneyi inali imodzi mwa mapulogalamu apadera osiyanasiyana omwe anakonzera alendo ochokera ku mayiko ena