Pitani ku nkhani yake

Ofesi ya nthambi yatsopanoyi ili ndi nyumba imodzi ya maofesi komanso nyumba 4 zogonamo

FEBRUARY 13, 2020
CAMEROON

Ntchito Yosamukira ku Ofesi ya Nthambi Yatsopano ku Cameroon Yatha

Ntchito Yosamukira ku Ofesi ya Nthambi Yatsopano ku Cameroon Yatha

Pa 20 January, 2020, banja la Beteli ku Cameroon linasamukira kumaofesi a nthambi atsopano omwe ali ku Logbessou kumpoto cham’mawa kwa mzinda wa Douala. Panopa, panthambi yatsopanoyi pali abale ndi alongo 59 omwe amakhalira pomwepo ndipo ena 71 amayendera.

Abale ndi alongo athu akutsitsa zinthu pamalo atsopanowa

Ofesi ya nthambi yakale inali m’dera la Bonaberi, kumadzulo kwa mzinda wa Douala. Nthambiyi inali ndi nyumba zimene zinakonzedwanso mu 1993. Apa n’kuti gulu lathu litavomerezedwanso pambuyo pa chiletso chomwe chinatenga zaka 23. Kungoyambira mu 1993, chiwerengero cha ofalitsa m’gawo la nthambi ya Cameroon chakula kwambiri, kuchoka pa 19,268 kufika pa 52,000 ndipo pofika pano, nthambiyi ikumasulira mabuku athu ndi zinthu zina m’zinenero 29. Chifukwa cha kuwonjezeka kumeneku, abale anaganiza zopezanso malo ena. *

Atumiki a pabeteli akugwira ntchito mu ofesi yatsopano m’Dipatimenti Yoona za Ndalama

M’tsogolomu, pa ofesi ya nthambiyi padzakhala malo omwe alendo azikaona zinthu zosiyanasiyana ndipo adzatsegulidwa chakumapeto kwa chaka cha 2020. Malowa adzakhala oonetsera zinthu zokhudza ntchito zimene zimagwiridwa pa nthambiyi komanso mbiri ya ntchito yolalikira ku Cameroon, Equatorial Guinea, ndi Gabon.

Chikwangwani cha m’Chingelezi komanso m’Chifulenchi chosonyeza kuti atumiki a pabeteli yatsopanoyi alandiridwa

M’bale Stephen Attoh wa m’Komiti ya Nthambi ya Cameroon anati: “Pa nthawi yomwe tinkasamukira ku nthambi yatsopanoyi tinkangoona ngati tikulota. Tinatsimikiza ndi mtima wonse kuti tipereka kwa Yehova zonse zomwe tingathe pomutumikira pamalo abwino kwambiri amenewa. Yehova watichitira zinthu zabwino kwambiri ndipo tikuyamikira mokondwera.”—Salimo 145:7.

^ Kuwonjezera pa dziko la Cameroon, ofesiyi imayang’aniranso ntchito yolalikira ku Equatorial Guinea ndi Gabon, komwe kuli mipingo 667.