Pitani ku nkhani yake

Chithunzichi chikusonyeza malo amene pakumangidwa ofesi ya nthambi yatsopano ndipo chinajambulidwa kuchokera m’mwamba. Maofesi ndi amene akuoneka pakona kumanja, ndipo nyumba 4 zogonamo ndi zimene zili kumanzere.

MARCH 22, 2019
CAMEROON

Ntchito Yomanga Ofesi ya Nthambi Yatsopano ku Cameroon Ikuyenda Bwino

Ntchito Yomanga Ofesi ya Nthambi Yatsopano ku Cameroon Ikuyenda Bwino

Tsopano padutsa chaka chiyambireni ntchito yomanga ofesi ya nthambi yatsopano ku Cameroon. Monga mmene chithunzi chili pamwambapa chikusonyezera, mbali zina za nyumba 4 zogonamo komanso maofesi zamangidwa kale. Paofesi ya nthambi yatsopanoyi pazidzakhala anthu 60 ndipo maofesi adzakhala ndi malo ogwirira ntchito anthu 71. Tikuganiza kuti ofesi ya nthambiyi idzayamba kugwiritsidwa ntchito chakumapeto kwa mwezi wa December 2019. Zithunzi zotsatirazi zikusonyeza mmene ntchito yomanga ofesiyi ikuyendera.

Mmene ofesi ya nthambiyi izidzaonekera ikadzatha kumangidwa

 

July 2018: Nyumba yomwe ikuoneka chakuno ndi Nyumba Yogona Yachitatu ndipo khoma la nyumbayi layamba kumangidwa.

August 2018: Mpanda udzamangidwa kuzungulira malo onsewa.

September 2018: Nyumba yomwe ikuoneka chakuno ndi Nyumba Yogona 4 ndipo idzakhala ya nsanjika. Mbali yoyamba yatha kumangidwa.

October 2018: Chithunzichi chikusonyeza pamene padzakhale khomo la pamalo olandirira alendo ku maofesi.

December 2018: Akuika denga la Nyumba Yogona Yachiwiri ndi Yachitatu.