Pitani ku nkhani yake

15 AUGUST, 2022
CAMEROON

Baibulo la Malemba Achigiriki Achikhristu Latulutsidwa M’Chiboulou

Baibulo la Malemba Achigiriki Achikhristu Latulutsidwa M’Chiboulou

Pa 6 August 2022, M’bale Gilles Mba wa m’Komiti ya Nthambi ku Cameroon, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Achigiriki Achikhristu m’Chiboulou pa pulogalamu yamsonkhano womwe unachita kujambulidwa. Ofalitsa anaonera msonkhano wochita kujambulidwawu pomwe panatulutsidwa Baibulo logwiritsa ntchito pazipangizo zamakono. Mabaibulo osindikizidwa akuyembekezeka kudzatuluka mu 2023.

Ofesi yomasulira mabuku m’Chiboulou yomwe ili ku Ebolowa m’dziko la Cameroon

Ngakhale kuti Mabaibulo ena a m’Chiboulou alipo, koma ndi okwera mtengo kwambiri. Mabaibulo ena amagwiritsa ntchito mawu achikale komanso anachotsamo dzina la Mulungu. Kuwonjezera apo, Mabaibulowa sanamasulire molondola mawu ambiri a m’Baibulo loyambirira. Mwachitsanzo, Mabaibulo ena a m’Chiboulou anamasulira mawu akuti “Ufumu wa Mulungu,” kuti “Mtundu wa Mulungu,” “Banja la Mulungu” kapena “Dziko la Mulungu.” Chifukwa chakuti Baibulo latsopanoli lagwiritsa ntchito mawu akuti “Ufumu,” kukhala kosavuta kulongosola kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lomwe Yehova anakhazikitsa.

Mmodzi wa ogwira ntchito yomasulira ananena kuti: “Pogwiritsa ntchito Baibuloli, tikwanitsa kuphunzitsa anthu ena zinthu zomwe ndi zolondola komanso zodalirika.”

Tili ndi chikhulupiriro chonse kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Achigiriki Achikhristu la m’Chiboulou lithandiza abale ndi alongo athu kuti apitirize kuthandiza “anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.