Pitani ku nkhani yake

10 OCTOBER, 2022
CAMEROON

Baibulo la Dziko Latsopano Lathunthu Latulutsidwa m’Chibasa cha ku Cameroon

Baibulo la Dziko Latsopano Lathunthu Latulutsidwa m’Chibasa cha ku Cameroon

Pa 1 October 2022, M’bale Stephen Attoh wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Cameroon, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la pazipangizo zamakono m’Chibasa cha ku Cameroon. Baibuloli analitulutsa pamsonkhano wochita kujambulidwa. Baibulo lochita kusindikizidwa lidzayamba kupezeka mu April 2023. Aka ndi koyamba kuti a Mboni za Yehova ku Cameroon amasulire Baibulo lonse m’chilankhulo cha anthu am’dzikoli. Mu 2019, a Mboni anatulutsa Baibulo la Malemba Achigiriki m’Chibasa cha ku Cameroon.

Ofesi yomasulira mabuku m’Chibasa yomwe ili ku Douala ku Cameroon

Baibuloli lisanatulutsidwe, pankapezeka Mabaibulo ena athunthu m’Chibasa. Komabe, Mabaibulowa amasowa, ndi okwera mtengo komanso muli mawu amene anthu ambiri anasiya kuwagwiritsa ntchito. Mmodzi mwa anthu omwe anamasulira Baibuloli, anati: “Baibulo latsopanoli lithandiza kuti anthu achidwi akhale ndi Baibulo lawolawo. M’Baibuloli muli mawu osavuta komanso amakono zomwe zithandize anthu kuti azilimvetsa bwino.”

Tikusangalala kuti abale ndi alongo athu omwe amalankhula Chibasa ali ndi Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu lomwe aziligwiritsa ntchito pophunzira paokha komanso mu utumiki akamafufuza anthu achidwi.—Mateyu 10:11.