Pitani ku nkhani yake

AUGUST 5, 2019
CAMEROON

A Mboni za Yehova ku Cameroon Atulutsa Baibulo Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chibassa

A Mboni za Yehova ku Cameroon Atulutsa Baibulo Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chibassa

Pamsonkhano wachigawo womwe unachitikira mumzinda wa Douala ku Cameroon pa 2 August, 2019, a Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la chinenero cha Chibassa. Ntchito yomasulira Baibulo la Malemba Achigiriki limeneli inatenga miyezi 18. Aka ndi koyamba kuti a Mboni za Yehova amasulire Baibulo m’chinenero chobadwira cha anthu a ku Cameroon.

M’bale Peter Canning wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Cameroon, anatulutsa Baibuloli pa tsiku loyamba la msonkhano wachigawo pa Malo a Msonkhano a Logbessou. Pamsonkhanowu panali anthu 2,015.

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Achigiriki lisanatulutsidwe m’chinenero chawo, abale ndi alongo olankhula Chibassa ankagwiritsa ntchito Baibulo lomwe linali lokwera mtengo kwambiri komanso lovuta kumva. Mmodzi mwa anthu omwe anagwira nawo ntchito yomasulira Baibulo la Malemba Achigiriki m’Chibassa anati: “Baibulo latsopanoli lithandiza ofalitsa kuti azimvetsa Baibulo mosavuta. Liwathandizanso kuti apitirize kukonda kwambiri Yehova komanso gulu lake.”

Ku Cameroon kuli anthu pafupifupi 300,000 olankhula Chibassa. M’gawo la nthambi ya Cameroon muli ofalitsa 1,909 olankhula Chibassa.

Tikukhulupirira kuti anthu akamawerenga Baibuloli, lomwe ndi lolondola komanso losavuta kumva, liwathandiza kuona kuti “mawu a Mulungu ndi amoyo.”—Aheberi 4:12.