Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 14, 2019
ARGENTINA

Mmene Ntchito Yomanga Ofesi ya Nthambi Ikuyendera ku Argentina

Mmene Ntchito Yomanga Ofesi ya Nthambi Ikuyendera ku Argentina

Chithunzi cha ofesi ya nthambi yatsopano ku Argentina chomwe chinajambulidwa dzuwa likulowa

Patha chaka ndi miyezi kuchokera pamene ntchito yomanga ofesi ya nthambi ku Argentina inayamba ndipo panopa ntchitoyi yatsala pang’ono kutha. Ofesi ya nthambi yatsopanoyi ili ndi nyumba zitatu. Nyumba imodzi ili ndi maofesi pomwe nyumba ziwiri ndi zokhalamo anthu, ndipo malowa kukula kwake ndi mamita 8,524 mbali zonse. Ntchito yomangayi ikuyembekezeka kudzatha mu July 2020.

Ndife osangalala ndi mmene ntchito yomanga ofesi ya nthambi yatsopano ku Argentina ikuyendera. Tikupemphera kuti Yehova apitirize kudalitsa ntchitoyi.—Deuteronomo 28:8.

 

Mu April 2019: Kaonekedwe ka maofesi. Zipilala zomwe zikuonekazo zikuyambira pansi pa nyumbayi ndipo zifika m’mwamba. Zimenezi zidzathandiza kuti nyumbayi idzakhale yolimba kwambiri

Mu June 2019: Wogwira ntchito yomanga wakwera pamwamba ndipo akumangirira chikombole chomwe adzathiremo konkire yopangira zipilala za Nyumba Yogona A

Mu July 2019: Ogwira ntchito yomanga akuika zitsulo zothiramo konkire komanso mawaya a magetsi pansi pa nsanjika yachitatu ya maofesi

Mu July 2019: Ogwira ntchito akuthira konkire pansi pa nsanjika yachiwiri ya Nyumba Yogona A. Nyumbayi idzakhala ya nsanjika 5 ndiponso khonde

Mu July 2019: Kaonekedwe ka malo oimika magalimoto m’galaja. Pansi pazidzakhala magalimoto 72 ndipo pamwamba pazidzakhalanso magalimoto 72

Mu August 2019: Nyumba Yogona A ndi B zikuoneka chakumanzere ndipo maofesi ali chakutsogoloko kumbuyo kwa namatcheni