AUGUST 7, 2019
ARGENTINA
Mlongo Cecilia Alvarez Wapangidwa Maopaleshoni 43 M’zaka 25 Popanda Kumuika Magazi
Mlongo Cecilia Alvarez yemwe kawo ndi ku Argentina, wakhala akudwala kwambiri kwa moyo wake wonse. Mlongoyu anapangidwa opaleshoni yoyamba atakwanitsa masiku 16 okha. Pa 18 May, 1994, madokotala ku Argentina anakonza mavuto okhudza msana wake omwe anachitika pamene ankabadwa. Kuchokera tsiku limenelo zomwe ndi zaka 25 zapitazo, Cecilia wapangidwa maopaleshoni enanso 42 ndipo ambiri mwa maopaleshoniwa anapangidwa ali mwana. Opaleshoni yaposachedwapa ndi imene anamupanga kumayambiriro a chaka chino yomwe inali yokonza mbali yamanzere ya chiuno chake. Mofanana ndi maopaleshoni omwe anamupanga m’mbuyomu, opaleshoniyi inachitika bwinobwino popanda kumuika magazi.
Cecilia anati: “Kupangidwa maopaleshoni ambirimbiri ndiponso kupatsidwa chithandizo cha mankhwala chosiyanasiyana kwakhala kukundisowetsa mtendere.” Komabe, iye wakhala akuyesetsa kuona vuto lake moyenera komanso kudalira Yehova. Kuonjezera pamenepo, iye wakhala akuyesetsa kwambiri kutsatira zimene madokotala akhala akumuuza, ndipo makolo ake akhala akumuthandiza kuchita zimenezi. Cecilia anati: “Kukonzekeretsa thupi langa opaleshoni isanachitike kunali kofunika kwambiri. Zimenezi zikuphatikizapo kumwa mankhwala komanso kudya zakudya zothandiza kuti thupi langa lipange maselo a magazi ofiira ambiri.”
Pofotokoza za magulu a zachipatala omwe amuthandiza pa zaka zonsezi, Cecilia anati: “Ndikuyamikira kwambiri ntchito yomwe anagwira, osati chabe chifukwa choti anapulumutsa moyo wanga, komanso chifukwa choti analemekeza zimene ndinanena zoti asandiike magazi.”
Madokotala omwe anagwira ntchito ndi Cecilia ananena kuti amalemekeza Cecilia komanso abale amene anamuthandiza. Dr. Ernesto Bersusky anali dokotala wamkulu wa matenda okhudza msana pachipatala cha Juan P. Garrahan Children’s Hospital ku Buenos Aires. Iwo anali m’gulu la madokotala omwe anapanga Cecilia maopaleshoni ambiri a msana. Iwo anati: “Pa nthawi yonse imene ndachita zinthu ndi Cecilia, ndaona kuti ndi wotsimikiza mtima kutsatira zomwe anasankha komanso amafotokoza momveka bwino zimene amakhulupirira. Ndakhala ndikuyankhula naye maulendo ambiri, kumufotokozera zimene ndikufuna kuchita ndiponso kumutsimikizira kuti saikidwa magazi.”
Dr. Susana Ciruzzi, yemwe ndi loya komanso membala wa komiti ya akatswiri oona za zinthu zoyenera ndi zosayenera pa nkhani ya zamankhwala pachipatala cha Juan P. Garrahan Children’s Hospital, anati: “Pakhala pali mgwirizano wabwino pakati a Mboni za Yehova ndi azachipatala. Monga madokotala, takhala tikugwira ntchito ndi a Mboni za Yehova ndipo tinagwirizana zosintha mmene timaganizira komanso njira zomwe timagwiritsa ntchito. Zimenezi zatithandiza kuti tipeze njira zina zothandizira odwala popanda kuwaika magazi.”
Kuwonjezera pa madokotala odziwa bwino ntchito yawo omwe anamuthandiza, Cecilia akuyamikiranso abale ndi alongo chifukwa choti anamuthandiza kwambiri. Iye anati: “Ndikuthokoza kwambiri ntchito yomwe abale a m’Komiti Yolankhulana ndi Achipatala komanso a m’Gulu Loyendera Odwala anagwira. Ngakhale kuti amafunikanso kusamalira mabanja awo komanso maudindo ena, iwo amadzimana zinthu zambiri komanso amapezeka nthawi iliyonse yomwe ndikuwafuna. Ndikuthokoza kwambiri thandizo lawo.”
Ngakhale kuti Cecilia yemwe panopa ali ndi zaka 25 amamva ululu nthawi zonse komanso amagwiritsa ntchito njinga ya olumala, iye amaona matenda ake moyenera. Iye anati: “Ndikukhulupirira kuti mavuto angawa andithandiza kuti ndisinthe umunthu wanga komanso andithandiza kuti ndikhale ndi makhalidwe a Chikhristu.”
Cecilia anapitiriza kunena kuti: “Nditangopangidwa opaleshoni ina, m’bale wa m’Komiti Yolankhulana ndi Achipatala anabwera kudzandiona ndipo anatchula lemba la Miyambo 10:22 lomwe limati: ‘Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu [wosatha].’ Lembali linandikhudza mtima kwambiri ndipo ndizilikumbukira nthawi zonse.”
Pa 1 May, 2019, mlongo wathu Cecilia analandira dalitso lapadera kwambiri pamene anavomerezedwa kuyamba kutumikira monga mpainiya wokhazikika. Apa zikuonekeratu kuti Yehova walimbitsa komanso kutonthoza mlongo wathu wokondedwayu. Zimenezi zachititsa kuti mlongoyu azisangalala kwambiri kulalikira kwa ena uthenga wotonthoza wopezeka m’Mawu a Mulungu.
Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kutonthoza tonsefe tikamakumana ndi mavuto osiyanasiyana ngati mmene wathandizira Cecilia.—2 Akorinto 1:4.