Pitani ku nkhani yake

Malo a Nkhani

 

2017-09-21

RUSSIA

A Mboni za Yehova Akuvutika Kwambiri Chifukwa cha Chigamulo cha Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia

Chigamulo cha khoti chachititsa kuti anthu ambiri azidana ndi a Mboni ndipo chapereka mphamvu kwa anthu komanso akuluakulu a boma kuti aziwachitira nkhanza.

2017-10-09

HAITI

Ntchito Yothandiza Anthu Omwe Anakhudziwa ndi Mphepo Yoopsa Yotchedwa Matthew ku Haiti Yatsala Pang’ono Kutha

Ntchito yothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi ikuyembekezereka kutha pofika mu June 2017.

2018-01-30

UNITED STATES

Amboni a ku United States Anapirira Mavuto Obwera Chifukwa cha Mphepo ya Mkuntho Yotchedwa Hurricane Harvey

A Mboni za Yehova ambiri omwe nyumba zawo zinaonongeka chifukwa cha mphepo ya mkuntho akulandira thandizo kudzera mu dongosolo lomwe linapangidwa lothandizira anthuwa.

2017-06-29

MALAWI

Ana Awiri a Mboni za Yehova Anawalola Kuyambiranso Sukulu Atawachotsa Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Ana awiri a Mboni za Yehova anawachotsa sukulu chifukwa chokana kuimba nawo nyimbo ya fuko. Akuluakulu a pasukulupo anawalola kuti ayambirenso sukulu.

2023-05-06

TAIWAN

Pulogalamu Yopereka Ntchito zina Kwa Anthu Okana Usilikali ku Taiwan Ikuyenda Bwino Kwambiri

Boma la Taiwan linapereka mwayi wogwira ntchito zina za boma kwa anthu okana usilikali.

2017-09-21

SOUTH KOREA

Khoti la ku South Korea Lamva Madandaulo a Anthu Okana Usilikali

Khoti linagamula kuti likulu la asilikali lisiye kufalitsa pawebusaiti yawo mayina, ma adiresi komanso zinthu zina zokhudza anthu omwe amakana usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira.