Pitani ku nkhani yake

Mfundo Zokhudza Kusunga Chinsinsi

Mfundo Zokhudza Kusunga Chinsinsi

ZOFUNIKA: MUKAMAGWIRITSA NTCHITO WEBUSAITI YATHU KAPENA KULEMBA ZINTHU ZOKHUDZA INUYO PAWEBUSAITIYI MUMASONYEZA KUTI MWAVOMEREZA ZOTI POGWIRITSA ZINTHUZO TIZITSATIRA MFUNDO ZIMENE TAFOTOKOZAZI KOMANSO MALAMULO ENA AMENE ANGAKHUDZE NKHANIYI.

 KUSUNGA CHINSINSI

Timayesetsa kuti tiziteteza zinthu zokhudza inuyo n’cholinga choti zisadziwike kwa anthu osayenera. Mfundo zotsatira zimene tifotokoze zikusonyeza mmene tidzagwiritsire ntchito zinthu zimene mwalemba zokhudza inuyo pawebusaiti yathu. Mukalowa pawebusaitiyi timasunga zinthu zina zokhudza inuyo ndipo tikudziwa kuti kuteteza zinthuzi n’kofunika kwambiri komanso timafuna kuti mudziwe zimene tidzachite ndi zinthuzo. Mwina mungafune kulemba zinthu zina zokhudza inuyo zomwe simukufuna kuti ena azione. Mawu oti “zinthu zokhudza inuyo” akunena za zinthu monga dzina lanu, imelo yanu, adiresi yanu kapena nambala yanu ya foni. Kuti mupite pamalo amene anthu onse angapite pawebusaiti yathu simuyenera kulemba zinthu zokhudza inuyo. Tikanena kuti “webusaiti yathu” tikunena za jw.org, tv.jw.org, stream.jw.org ndi wol.jw.org.

 KUGWIRITSA NTCHITO ZINTHU ZOKHUDZA INUYO

Webusaiti yathuyi ndi ya bungwe la Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. (“Watchtower”), lomwe lili ku New York ndipo silichita zamalonda. Bungweli limayendetsa ntchito zosiyanasiyana zimene a Mboni za Yehova amachita kuphatikizapo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Mukatsegula akaunti, kupereka ndalama, kupempha phunziro la Baibulo kapena kuchita zinthu zina zimene zimafuna kuti mulembe zinthu zokhudza inuyo, mumasonyeza kuti mwavomereza mfundo zotsatira zimene tifotokoze. Mumasonyezanso kuti mwavomereza kuti zinthu zokhudza inuyozo zisungidwe m’makompyuta a ku United States, zitumizidwe kumalo oyenera komanso zigwiritsidwe ntchito ndi Watchtower kapena mabungwe athu ena amene amayendetsa ntchito za Mboni za Yehova kumayiko ena n’cholinga choti zimene mukufunazo zichitike. Gulu la Mboni za Yehova limagwiritsa ntchito mabungwe osiyanasiyana padziko lonse pogwira ntchito yake. Gululi lingagwiritse ntchito mipingo ya Mboni za Yehova, maofesi a nthambi kapena mabungwe athu ena.

Zinthu zokhudza inuyo zimene mwalemba pawebusaiti yathu zimagwiritsidwa ntchito mogwirizana ndi cholinga chanu polemba zinthuzo. Mwachitsanzo, ngati mwalemba zinthuzo popereka ndalama ku bungwe limene a Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito m’dziko lanu, zinthuzo zimagwiritsidwa ntchito ndi bungwe limenelo. Kapena ngati mwapempha phunziro la Baibulo, dzina lanu komanso zinthu zina zimene mwalemba zimagwiritsidwa ntchito ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu komanso mpingo wa Mboni za Yehova wa m’dera lanu.

Ngati dziko limene mumakhala lili ndi malamulo oteteza zinthu zokhudza anthu, mungapite pamene palembedwa Maadiresi a Odziwa Malamulo Oteteza Zinthu Zokhudza Anthu.

 KUTETEZA ZINTHU ZOKHUDZA INUYO

Timaona kuti kuteteza zinthu zokhudza inuyo ndi kofunika kwambiri. Timagwiritsa ntchito njira zamakono poteteza zinthu zanu kuti anthu osayenera asamazione, zisamagwiritsidwe ntchito molakwika, zisamasinthidwe mosayenera komanso kuti zisamawonongedwe kapena kusowa. Anthu onse amene amagwiritsa ntchito zinthu zanuzi avomera kuti aziziteteza komanso kuzisunga mwachinsinsi. Timangosunga zinthu zokhudza inuyo kwa nthawi imene ingafunike kuti tichite zimene mukufunazo komanso kuti titsatire malamulo okhudza nkhaniyi.

Timateteza zinthu zanu tikamazitumizira kwina pochititsa kuti zinthuzo zikhale zosawerengeka ndipo timagwiritsa ntchito pulogalamu ngati Transport Layer Security (TLS). Timatetezanso zinthu zanu pogwiritsa ntchito mapulogalamu omwe anthu ambiri sadziwa mmene amagwirira ntchito ndipo amasungidwa m’malo otetezeka kwambiri. Timatsatira malamulo okhwima poteteza zinthuzi.

 ANA

Ngati simunafike msinkhu woti m’dziko lanu boma limaona kuti ndinu wodziimira payekha, mungalembe zinthu zokhudza inuyo pawebusaitiyi pokhapokha ngati makolo anu kapena munthu wina wokuyang’anirani wavomereza. Ngati ndinu makolo kapena amene akuyang’anira mwanayo ndipo mwavomereza kuti alembe zinthu zokhudza iyeyo pawebusaitiyi, ndiye kuti mwavomera mfundo zimene tafotokozazi.

 MAWEBUSAITI ENA

Nthawi zina mungapeze malo apawebusaitiyi amene amakulumikizani ndi mawebusaiti ena omwe timagwiritsa ntchito kuti azitichitira zinthu zina monga kulemba mafomu a pa intaneti. Mungadziwe kuti mwafika pawebusaiti ina chifukwa imaoneka mosiyana ndi webusaiti yathu komanso adiresi imene ikuoneka papulogalamu yolowera pa intaneti imasintha. Tisanayambe kugwiritsa ntchito mawebusaiti ena timatsimikizira kaye kuti amayendera mfundo zofanana ndi zimene timayendera poteteza zinthu zokhudza anthu ndipo nthawi zina timatsimikiziranso kuti akuchitabe zimenezi. Ngati mukufuna kudziwa mfundo zimene webusaiti inayake imagwiritsa ntchito pa nkhaniyi, mungazipeze pawebusaitiyo.

 KUDZIWITSA ANTHU MFUNDOZI ZIKASINTHA

Nthawi zonse timayesetsa kukonzanso webusaiti yathu kuti izikhala yabwino kwambiri komanso yosavuta kuigwiritsa ntchito. Chifukwa cha zimenezi komanso chifukwa choti malamulo ndi zinthu zokhudza makompyuta zimasintha, zimene timachita poteteza zinthu zokhudza anthu nthawi zina zimasinthanso. Tikasintha mfundo zimene timayendera timalemba zimene tasintha pawebusaiti yathu kuti mudziwe mmene timasungira komanso kugwiritsira ntchito zinthu zokhudza inuyo.

 KUGWIRITSA NTCHITO SCRIPTING KAPENA JAVASCRIPT

Timagwiritsa ntchito Scripting kuti webusaiti yathu izigwira bwino ntchito. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti webusaitiyi izionetsa zinthu zimene mukufuna mofulumira. Koma sitigwiritsa ntchito Scripting kuti tiike mapulogalamu pakompyuta yanu kapena titenge zinthu zokhudza inuyo popanda chilolezo chanu.

Kuti mbali zina za webusaiti yathu zizigwira bwino ntchito, muyenera kuonetsetsa kuti JavaScript ndi yotsegula m’pulogalamu yanu yolowera pa intaneti. Mapulogalamu ambiri olowera pa intaneti amakupatsani mwayi wotsegula kapena kutseka JavaScript pamawebusaiti ena. Mungawerenge zokuthandizani (Help) papulogalamu yanu yolowera pa intaneti kuti mudziwe mmene mungatsegulire Scripting pamawebusaiti ena.