Pitani ku nkhani yake

‘Anachita Zinthu Moona Mtima’

‘Anachita Zinthu Moona Mtima’

Danielle yemwe ndi wa Mboni za Yehova ndipo amakhala ku South Africa, anatola chikwama chomwe munthu wina anaiwala mu shopu ya khofi. M’chikwamamo anapezamo kachikwama ka ndalama momwe munalinso makadi a ku banki. Danielle ankafunitsitsa kupereka chikwamacho kwa mwiniwake choncho anafufuza adiresi ndi nambala ya foni koma anangopezamo dzina la bambo yemwe anataya chikwamacho. Kenako anayesa kufufuza zokhudza bamboyo ku banki yake koma sizinathandize. Ndiyeno Danielle anaimbira foni dokotala wina pa nambala yomwe anaipeza pa lisiti lomwe linali m’chikwamamo. Munthu wogwira ntchito pamalo olandirira alendo anayankha foniyo ndipo anavomera kupereka nambala ya Danielle kwa bamboyo.

Bamboyo anadabwa kwambiri atalandira foni kuchokera ku ofesi ya dokotala wake yomuuza kuti Danielle wapeza chikwama chake ndipo akufuna kumupatsa. Atapita kukatenga chikwamacho anakumana ndi Danielle ndi bambo ake. Iwo anagwiritsa ntchito mpata umenewo kuuza bamboyo chifukwa chake ankafunitsitsa kuti akumane naye. Iwo anafotokoza kuti monga a Mboni za Yehova, amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo. N’chifukwa chake amayesetsa kuchita zinthu moona mtima nthawi zonse.—Aheberi 13:18.

Patadutsa maola angapo, Bamboyo anatumiza uthenga woyamikiranso Danielle ndi bambo ake chifukwa chomubwezera chikwama chake ndi kachikwama ka ndalama. Iye analemba kuti: “Ndikukuthokozani kwambiri chifukwa choyesetsa mwakhama kuti mundipeze. Ndinasangalala kwambiri kukumana nanu ndipo sindidzaiwala khalidwe labwino lomwe munalisonyeza. Ndiye pofuna kusonyeza kuyamikira, ndakutumizirani kangachepe. Ndikudziwa kuti mumadzipereka ndi mtima wonse kuti muzitumikira Mulungu. Kuona mtima ndi kukhulupirika kwa Danielle ndi umboni wakuti ndinu anthu abwino kwambiri. Ndikubwerezanso kuti zikomo kwambiri ndipo Mulungu adalitse utumiki wanu.”

Patapita miyezi ingapo, bamboyu analankhulananso ndi bambo a Danielle ndipo anawafotokozera zomwe zinamuchitikira, nayenso atatola chikwama cha ndalama. Iye ananena kuti tsiku lina atapita kukagula zinthu anapeza kachikwama pansi. Atapeza mayi yemwe anataya kachikwamaka anafotokozera mayiyo zomwe zinamuchititsa kuti amufunefune n’kumupatsa kachikwamako. Anafotokoza kuti anachita zimenezi chifukwa chakuti munthu winanso anamubwezera kachikwama kake katasowa. Iye anati: “Munthu akachitira wina zinthu moona mtima komanso mokoma mtima, zimathandiza kuti anthu enanso azichitirana zinthu moona mtima ndipo anthu ambiri amasangalala.”