Pitani ku nkhani yake

Anakhalabe Okhulupirika Atakumana ndi Mayesero

Onani mmene Mawu a Mulungu amathandizira a Mboni za Yehova kukhalabe okhulupirika akakumana ndi mayesero.

Nyumba Imene Munayesedwera Chikhulupiriro cha a Mboni Ena

Nyumba ya ku Spain yomwe inali ndende ya a Mboni za Yehova ambirimbiri omwe anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Sitinalole Kusiya Zimene Timakhulupirira

Daniel Lokollo amakumbukira mmene olondera ndende anamuzunzira.

Sanasiye Kutumikira Yehova Ngakhale Kuti Ankaopsezedwa

Kodi anthu ankaona bwanji nkhanza zimene anthu ena ankachitira a Mboni za Yehova ku Georgia?

Ndine Msilikali wa Khristu

Demetrius Psarras anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Komabe anapitiriza kuthandiza kuti Mulungu atamandike ngakhale atakumana ndi mayesero oopsa.

Anaphunzira kwa Akaidi

Ali m’ndende ku Eritrea, munthu wina anadzionera yekha kuti a Mboni amachita zimene amaphunzitsa ena pamoyo wawo.

Ankabisa Notsi Pansi pa Mashini Ochapira Zovala

Mayi wina anagwiritsa ntchito njira yatsopano pophunzitsa ana ake aakazi mfundo za m’Baibulo.

A Mboni za Yehova Anayankha Modekha Atakumana ndi Ansembe Olusa

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikhala odekha ngakhale pamene ena atiputa. Kodi malangizo amenewa ndi othandiza?

“Ufumu wa Mulungu Si Nkhambakamwa”

Efraín De La Cruz anatsekeredwa m’ndende 7 ndiponso kumenyedwa koopsa chifukwa cholalikira uthenga wabwino. N’chiyani chinamuthandiza kuti azilalikira mwakhama kwa zaka zoposa 60?

Mpainiya Wopanda Mantha

M’bale André Elias anatumikira kwa zaka 60 ndipo anakhalabe wokhulupirika pa nthawi imene ankafunsidwa mafunso komanso kuopsezedwa.

Tsopano Ndili pa Mtendere ndi Mulungu Komanso Amayi Anga

Pamene Michiyo Kumagai anasiya kulambira makolo akale, amayi ake anasiya kugwirizana naye. Kodi Michiyo anachita zotani kuti ayambenso kugwirizana nawo?