Pitani ku nkhani yake

Baibulo Limasintha Anthu

Moyo Wosangalala

Ndinapeza Chuma Chenicheni

Kodi munthu yemwe bizinesi yake inkamuyendera kwambiri anapeza bwanji chuma chamtengo wapatali kuposa ndalama?

Juan Pablo Zermeño: Yehova Anandithandiza Kukhala ndi Moyo Watanthauzo

Mavuto aakulu amene takumana nawo pamoyo wathu angatikhudze kwa moyo wathu wonse. Juan Pablo ali mwana anakumana ndi mavuto akuluakulu. Onani zimene zinamuthandiza kuti akhale ndi moyo watanthauzo, wamtendere komanso wosangalala.

Kodi Chikondi Komanso Kukhulupirika Zidzagonjetsa Liti Chidani?

N’zovuta kusiya mtima wodana ndi anthu a mtundu wina. Koma taonani zimene Myuda wina komanso munthu wina wa ku Palesitina anachita.

Ndinapeza Mayankho Ogwira Mtima a Mafunso Anga

Ernest Loedi anapeza mayankho ogwira mtima a mafunso ake. Mayankho a m’Baibulo anamuthandiza kukhala ndi chiyembekezo.

Mafunso Atatu Omwe Anasintha Moyo Wanga

Mphunzitsi anaphunzitsidwa ndi mwana wake wasukulu. Doris Eldred anapeza mayankho ogwira mtima a mafunso ake.

Sindinkafuna Kufa

Yvonne Quarrie ankafuna kudziwa cholinga chimene Mulungu anamulengera. Yankho la funsoli linamuthandiza kuti asinthe moyo wake.

Yehova Wandichitira Zazikulu

Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zinathandiza Crystal, yemwe ankachitidwa nkhanza zokhudza kugonana ali wamng’ono, kuti akhale paubwenzi ndi Yehova ndiponso kudziwa kuti moyo wake ndi wofunika kwambiri?

Ndinasiya Kudziona Ngati Wosafunika

Werengani nkhaniyi kuti muone zomwe a Israel Martínez anachita kuti athane ndi mtima wodziona ngati wosafunika.

Jeson Senajonon: Yehova Anandiyankha

Jeson sanalephere kukhala pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa cha vuto lake losamva.

Ndinagwirizana ndi Bambo Anga Patatha Zaka Zambiri

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake a Renée anayamba kuledzera komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo onani zimene zinawachititsa kuti asiyiretu makhalidwe oipawa.

Panopa Ndimaona Kuti Ndingathe Kuthandiza Ena

Julio Corio anachita ngozi ndipo ankaona kuti Mulungu samuganizira. Lemba la Ekisodo 3:7 linamuthandiza kuti asinthe maganizo.

Ndinali Munthu Wodzikonda Kwambiri

Christof Bauer ankawerenga Baibulo ali m’boti pakati pa nyanja ya Atlantic. Kodi anaphunzira zotani?

Ndinkafunitsitsa Kuthana ndi Kupanda Chilungamo

Rafika analowa m’gulu la anthu ofuna kuthana ndi zinthu zopanda chilungamo. Koma anaona kuti m’Baibulo muli lonjezo loti ndi Ufumu wa Mulungu wokha womwe udzabweretse mtendere komanso chilungamo padzikoli.

“Panopa Ndilibenso Maganizo Ofuna Kusintha Zinthu M’dzikoli”

Kodi Baibulo linathandiza bwanji munthu wina womenyera ufulu wa anthu ndi zinyama kudziwa chimene chingathandizedi kusintha zinthu padzikoli?

Ndinasiya Usilikali

Onani mmene mfundo za m’Baibulo zinathandizira Cindy kuti asinthe moyo wake wankhanza.

Ndinkaona Kuti Kulibe Mulungu

Kodi zinatheka bwanji kuti munthu amene kuyambira ali mwana ankatsatira mfundo zachikomyunizimu komanso mfundo yoti kulibe Mulungu, asinthe n’kuyamba kuphunzira Baibulo?

Kusintha Zimene Mumakhulupirira

“Ndinali Ndi Mafunso Ambiri”

N’chiyani chinathandiza a Mario omwe poyamba anali m’busa kuyamba kukhulupirira kuti a Mboni za Yehova amaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo?

Baibulo Linandithandiza Kupeza Mayankho a Mafunso Anga

Mayli Gündel anasiya kukhulupirira zoti kuli Mulungu bambo ake atamwalira. N’chiyani chinamuthandiza kuyambanso kukhulupirira zoti kuli Mulungu komanso kukhala ndi mtendere wamumtima?

Ankagwiritsa Ntchito Baibulo Poyankha Funso Lililonse

Isolina Lamela anali sisitere wakatolika koma anakhumudwa ndi zochita za magulu onse awiri. Kenako anakumana ndi a Mboni za Yehova amene anamuthandiza pogwiritsa ntchito Baibulo kuti adziwe chifukwa chake Mulungu anatilenga.

Anapeza “Ngale . . . Yamtengo Wapatali”

Mlongo Kennedy ndi M’bale Björn, anapeza choonadi chonena za Ufumu m’njira zosiyana kwambiri. Kodi zomwe anaphunzira zinasintha bwanji moyo wawo?

Ndinasiya Kupita Kuchipembedzo Chilichonse

Tom ankafunitsitsa kuti azikhulupirira Mulungu koma anakhumudwa ndi zochita komanso miyambo yachabechabe ya chipembedzo. Kodi kuphunzira Baibulo kunamuthandiza bwanji kuti akhale ndi chiyembekezo?

“Yehova Sanandiiwale”

Mzimayi wokonda kupemphera ameneyu anapeza mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso oti, N’chifukwa chiyani anthufe timafa? komanso, N’chiyani chimachitika tikamwalira? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene moyo wake unasinthira atadziwa zinthu zolondola.

”Ndinkafuna Kudzakhala Wansembe”

Kuyambira ali mwana, Roberto Pacheco ankafunitsitsa kudzakhala wansembe wa Katolika. Werengani kuti mudziwe zomwe zinachititsa kuti zinthu zisinthe pa moyo wake.

“Ankafuna Kuti Ndione Ndekha Kuti Zoona Ndi Ziti”

Luis Alifonso ankafuna kudzakhala mmishonale wa chipembedzo cha Mormon. Kodi kuphunzira Baibulo kunamuthandiza bwanji kuti asinthe zolinga zake komanso moyo wake?

Mankhwala Osokoneza Bongo Komanso Mowa

“Si Inenso Kapolo wa Chiwawa”

Tsiku limene ankayamba ntchito yake yatsopano, Michael Kuenzle anafunsidwa kuti, “Kodi ukuganiza kuti Mulungu ndi amene amachititsa mavuto padzikoli?” Funso limeneli linachititsa kuti ayambe kusintha moyo wake.

Moyo Wanga Unkangoipiraipirabe

Solomone ankaganiza kuti akasamukira ku United States, azikakhala ndi moyo wabwino. M’malo mwake, anayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo anamangidwa. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti asinthe moyo wake?

Misewu Ndi Imene Inali Nyumba Yanga

Zimene Antonio anakumana nazo pamoyo pamene ankachita zachiwawa, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, komanso kumwa mowa mwauchidakwa zinamuchititsa kuganiza kuti moyo wake unalibe phindu lililonse. Kodi n’chiyani chinamupangitsa kusintha maganizo ake?

Ndinayamba Kulemekeza Akazi Komanso Kudzilemekeza

Joseph Ehrenbogen anawerenga mfundo za m’Baibulo ndipo zinamuthandiza kusintha moyo wake.

“Ndinayamba Kuganizira Kwambiri za Moyo Wanga”

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene Baibulo linathandizira munthu wina kusiya makhalidwe oipa komanso maganizo ake kuti ayambe kusangalatsa Mulungu.

Khalidwe Langa Loipa Linanditopetsa

Dmitry Korshunov anali chidakwa, koma kenako anayamba kuwerenga Baibulo tsiku lililonse. Kodi n’chiyani chimene chinamuthandiza kuti asinthe khalidwe lake n’kukhala munthu wosangalala

“Ndinapeza Ufulu Weniweni”

Werengani kuti mudziwe mmene Baibulo lathandizira mnyamata wina kusiya kusuta fodya, mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa mwauchidakwa.

Kuphwanya Malamulo Komanso Zachiwawa

“Zochita Zanga Zoipa Komanso Kukonda Ndalama Zinandibweretsera Mavuto Ambiri”

Artan atatulutsidwa m’ndende anazindikira kuti zimene Baibulo limanena zokhudza ndalama ndi zoona.

“Ndinkadzikumbira Ndekha Manda”

N’chiyani chinathandiza munthu amene poyamba anali m’gulu la zigawenga ku El Salvador, kusintha moyo wake?

Panopa Ndimaona Anthu Mosiyana

A Sobantu anaphunzira mfundo zoona za m’Baibulo, anasiya moyo wachiwawa. Panopa amaphunzitsa anthu zokhudza dziko latsopano lopanda zachiwawa ndi uchigawenga.

Sindinkachedwa Kupsa Mtima

A Cristóbal Díaz omwe poyamba anali chigawenga amakhulupirira kuti mmene moyo wawo ulili panopa ndi umboni wakuti Baibulo lili ndi mphamvu zotha kusintha munthu. Panopa amasangalala kuti ali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.

Ndinali Mnyamata Wovuta Komanso Wokonda Ndewu

Kodi n’chiyani chinathandiza munthu wokonda ndewu wa ku Mexico kuti asinthe?

Ndithandizeni Kuti Ndikhaleko Mosangalala Komanso Mwamtendere kwa Chaka Chimodzi Chokha

Lemba la 1 Yohane 1:9, linamuthandiza kwambiri Alain Broggio.

Ndinkaona Ngati Zinthu Zikundiyendera

A Pawel Pyzara anali munthu wa makhalidwe oipa komanso ankafuna ntchito yapamwamba. Koma tsiku lina anasintha atamenyedwa ndi anthu 8

Moyo Wanga Unkangoipiraipirabe

Stephen McDowell anali wachiwawa, koma anthu ena atapha munthu, zinapangitsa kuti asinthe moyo wake.

Ndinaphunzira Kuti Yehova Ndi Wachifundo Komanso Amakhululuka

Normand Pelletier ankakonda kubera anthu mwachinyengo moti ankalephera kusiya. Koma tsiku lina analira kwambiri atawerenga vesi lina la m’Baibulo.

Ndinkamenya Nkhondo Yangayanga Yolimbana Ndi Kupanda Chilungamo Komanso Chiwawa

Antoine Touma anali katswiri wa Kung Fu, koma lemba la 1 Timoteyo 4:8 linamuthandiza kuti asinthe.

Ndinkayenda ndi Mfuti Kulikonse

Annunziato Lugarà anali wachiwawa, wakuba komanso chigawenga choopsa.

“Anthu Ambiri Ankadana Nane”

Werengani nkhaniyi kuti muone mmene kuphunzira Baibulo kunathandizira munthu yemwe anali wankhanza kusintha n’kukhala munthu wokonda mtendere.

Masewera, Nyimbo ndi Zosangalatsa

Zinkaoneka Ngati Zinthu Zikundiyendera

A Stéphane anali woimba wotchuka. Ngakhale ankaoneka kuti zinthu zikumuyendera, analibe mtendere wamumtima. Kodi anatani kuti akhale ndi moyo wabwino komanso wosangalala?

Mphotho Yaikulu Kwambiri pa Moyo Wanga

Kodi n’chiyani chinathandiza katswiriyu kuti asinthe n’kuyamba kutsatira mfundo za m’Baibulo?

“Ndinkakonda Kwambiri Karati”

Tsiku lina, Erwin Lamsfus anafunsa mnzake kuti, “Kodi unayamba waganizirapo kuti cholinga cha moyo ndi chiyani?” Zimene anamuyankha zinasintha moyo wake.

Ndinasintha Khalidwe Langa Movutikira Kwambiri

Kodi munthu wina anapeza bwanji mtendere wamumtima atasiya khalidwe loonera zolaula?

”Ndinali Munthu Wachiwawa”

Ngakhale kuti zinthu zinkamuyendera bwino pa nkhani ya zoimba, Esa ankaonabe kuti moyo wake ulibe phindu. Werengani kuti mumve mmene munthu wokonda nyimbo zaphokoso ameneyu anapezera moyo wosangalaladi.

Kutumikira Yehova Kumathandiza Kwambiri

Lemba lina linathandiza Hércules kuzindikira kuti akhoza kusintha khalidwe lake lankhanza n’kuyamba kumachita zinthu mwamtendere komanso mwachikondi kwambiri.

Ndinkakonda Kwambiri Masewera a Baseball Kuposa Chilichonse

A Samuel Hamilton ankakonda kwambiri masewera a Baseball koma atayamba kuphunzira Baibulo anasintha.

Lonjezo la Paradaiso Linasintha Moyo Wanga

Ivars Vigulis anali katswiri wa mpikisano woyendetsa njinga yamoto. Kodi ataphunzira Baibulo anayamba kuiona bwanji ntchito yakeyi?